-
Genesis 19:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pageti la mzinda wa Sodomu. Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 2 Ndiyeno anati: “Chonde ambuye anga, tiyeni kunyumba ya kapolo wanu. Tikakusambitseni mapazi ndiponso mukagone, kuti mawa mulawirire nʼkupitiriza ulendo wanu.” Koma iwo anati: “Ayi, ife tigona mʼbwalo lamumzindawu usiku wa lero.” 3 Ndiyeno Loti anawaumiriza kwambiri moti iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando, nʼkuwaphikira mkate wopanda zofufumitsa, ndipo anadya.
-