6 Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lengeza mofuula!”
Wina akufunsa kuti: “Ndilengeze mofuula za chiyani?”
“Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira.
Chikondi chawo chonse chokhulupirika chili ngati duwa lakutchire.+
7 Udzu wobiriwirawo umauma
Ndipo maluwawo amafota,+
Chifukwa mpweya wa Yehova umauzira zinthu zimenezi.+
Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.
8 Udzu wobiriwira umauma,
Maluwa amafota,
Koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka kalekale.”+