-
1 Timoteyo 1:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukulangiza kuchita zimenezi mogwirizana ndi maulosi amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+ 19 Ukhale ndi chikhulupiriro komanso chikumbumtima chabwino+ chimene anthu ena asiya kuchitsatira, moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa.
-
-
1 Timoteyo 6:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Menya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro. Gwira mwamphamvu moyo wosatha umene anakuitanira. Paja unalengeza momveka bwino zokhudza moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri.
-