-
Yeremiya 51:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Babulo anali ngati kapu yagolide mʼdzanja la Yehova.
Anachititsa kuti dziko lonse lapansi liledzere.
Mitundu ya anthu yaledzera ndi vinyo wake.+
Nʼchifukwa chake mitundu ya anthu ikuchita zinthu ngati anthu amisala.+
8 Babulo wagwa mwadzidzidzi ndipo wasweka.+
Mulirireni mofuula.+
Mʼpatseni mafuta a basamu kuti ululu wake uthe, mwina angachire.”
-
-
Chivumbulutso 17:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7 aja,+ anabwera nʼkundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetse chiweruzo cha hule lalikulu limene lakhala pamadzi ambiri,+ 2 limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo chiwerewere,*+ ndipo linaledzeretsa anthu amene akukhala padziko lapansi ndi vinyo wa chiwerewere* chake.”+
-
-
Chivumbulutso 18:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo amene ziwanda zimakhala. Wakhalanso malo amene mzimu uliwonse wonyansa* komanso mbalame iliyonse yonyansa ndi imene imadedwa zimabisala.+ 3 Iye wamwetsa mitundu yonse ya anthu vinyo wa chilakolako chake cha* chiwerewere.*+ Ndipo mafumu a dziko lapansi anachita naye chiwerewere.+ Amalonda* apadziko lapansi analemera chifukwa cha zinthu zambiri zamtengo wapatali zimene mkazi ameneyu anadziunjikira mopanda manyazi.”
-