-
Chivumbulutso 1:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi ndipo anali atamanga lamba wagolide pachifuwa. 14 Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera ngati ubweya woyera wa nkhosa, zinali zoyera kwambiri, ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.+ 15 Mapazi ake anali ngati kopa* woyengedwa bwino+ amene akunyezimira mʼngʼanjo ndipo mawu ake ankamveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.
-