Mmene Ukwati Umodzi Unapulumutsidwira
“Kugwiritsira ntchito uphungu wopezedwa mu bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu Wabanja Kukhala Wachimwemwe kunapulumutsa ukwati wanga,” analemba motero m’ŵerengi woyamikira kuchokera ku South Africa. “Mutu 5, ‘Mkazi Amene Ali Wokondedwa Kwambiri,’ unatsegula maso anga. Sindinalingalirepo m’maloto anga a akulu kuti ndingapangitse mavuto ambirimbiri popanda kulingalira. Ndikuyamikani kwenikweni. Ukwati wanga unali m’mbali za namondwe zenizeni za nyanja, ndipo tsopano, pambuyo pa miyezi ingapo, iwo wabwereranso kudokho lachimwemwe.”
Ngati mufuna thandizo la kupangitsa ukwati wanu kukhala wachimwemwe, inu mungapindule kuchokera ku bukhu limeneli. Landirani kope limodzi mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kali pansipa.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Kupangitsa Moyo Wanu Wabanja Kukhala Wachimwemwe. Ndatsekeramo K8.00.