Tsamba 2
Pali kusiyana kokulira mu ntchito ya za umoyo wabwino komwe kulipoo kuzungulira dziko lonsi. M’malo ena izi ziri zakuya ndi zopambana mwasayansi. M’mbali zina za dziko, samapeza zofunika zenizeni, kapena kuti zofunikazo sizimakhalako. Komabe, ngakhale pamene ntchito za umoyo wabwino zakulitsidwa kwenikweni, izo zimabwererabe m’mbuyo m’kuchinjiriza kuphatikizaponso kuchiritsa matenda.
Kodi ntchito zaumoyo zazikulu zidzakhalapo kwa onse mtsogolo mowonedweratu? Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chiripo kaamba ka kuchiritsa kotheratu ndi kuchinjirizidwa kotheratu kwa matenda onse?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Washington, D.C., General Hospital
WHO/UNICEF photo