Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 11/8 tsamba 19-21
  • Kodi Ndingapeze Bwanji Chisangalalo Monga Mwana Yekha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingapeze Bwanji Chisangalalo Monga Mwana Yekha?
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yesani Kumvetsetsa Nchifukwa Ninji
  • Sinthani Zoipa Kukhala Zabwino
  • Lingalirani za Ena
  • Tsatirani Zitsanzo Zabwino
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Muzithandiza Ana Anu Kulimbitsa Chikhulupiriro Chawo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 11/8 tsamba 19-21

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingapeze Bwanji Chisangalalo Monga Mwana Yekha?

“NDIMACHIDA ICHO. Ndimachida icho,” analira tero Sue Ann wa zaka zakubadwa 16. Koma Al, wocheperapo ndi zaka ziŵiri, ananena kuti: “Ndimakonda kukhala mwana yekha.”

Onse aŵiri, ndithudi, anali ndi zifukwa zawo. Koma kodi chiri chifukwa chakuti Sue Ann anali kugogomezera mopambanitsa kuipa kwake, pamene kuli kwakuti Al kwakukulukulu anali kuwona ubwino wake? Kodi inu—makamaka ngati muli mwana yekha—mumawona bwanji nkhaniyo? Kodi mumadzimva monga Sue Ann kapena monga Al? Kapena mochepera monga onse aŵiri?

Yesani Kumvetsetsa Nchifukwa Ninji

Banja la mwana mmodzi siliri mkhalidwe wa dziko. Koma mlingo wa obadwa m’maiko ena, makamaka mu North America ndi Europe, watsika kwambiri chakuti kukhala mwana yekha kudzakhala kwa ana mamiliyoni ambiri omwe akubadwa tsopano. Ndipo mu China, kumene chiyambire 1979 akhala ndi programu yaikulu ya kuletsa kubala, pali kuyerekezera kwa mabanja mamiliyoni 35 okhala kokha ndi mwana mmodzi. Pamene kuli kwakuti ana ena angapeze mkhalidwewo kukhala wovuta kuulandira, Elke, mkazi wachichepere yemwe anakula monga mwana yekha, akunena kuti kudziŵa chifukwa chake kunamuthandiza iye. “Ndinamvetsetsa zifukwa za makolo anga,” iye akulongosola, “ndipo ndiganiza kuti ichi chiri chofunika kuti mwana yekha akhale wosangalala ndi wokwaniritsidwa.”

Zifukwa zake zingakhale za mayanjano, zogwirizana ndi umoyo, kapena za mkhalidwe wina waumwini. Kapena chingangokhala kokha kaamba ka chifukwa cha zandalama. Kodi mumadziŵa, mwachitsanzo, kuti mu Great Britain kapena United States zowonongedwa za kulera mwana kufika ku uchikulire zingapitirire bwino lomwe pa $100,000? Chulukitsani ichi ndi 2, 3, kapena 4, ndipo mungamvetsetse chifukwa chimene makolo ena amanena kuti ‘mmodzi ali wokwanira.’

Chirichonse chimene chingakhale chifukwa, mwana yekha safunikira kukhumudwitsidwa ponena za mtsogolo mwake. Phunziro lofalitsidwa mu 1954 ndi ophunzitsa Cutts ndi Moseley linavumbula kuti lingaliro la kukhala ndi mwana mmodzi mwachiwonekere silimatembenukira kukhala losiyana ndi ena. Ndipo posachedwapa kwambiri, Dr. Alice Loomer, akumalemba mu Parents’ Magazine, ananena kuti ngakhale kuti kukhala mwana wobadwa yekha kudzamuyambukira iye, “chimene chimadetsa nkhaŵa koposa nsonga imodzi ya ‘kukhala wobadwa yekha’ chiri mmene mikhalidwe yonse ya umoyo wa anthu achichepere imagwirizanirana kumupangitsa iye munthu wapadera amene ali.”

Ndithudi simungasinthe mkhalidwe wanu, chotero chinsinsi cha chisangalalo chimakhala mu kusangalala ndi maubwino a kukhala mwana wobadwa yekha, pamene mukunyalanyaza kuipa kwake. Ngakhale kuposerapo, yesani kupindula kuchokera mu zoipazo. Motani?

Sinthani Zoipa Kukhala Zabwino

KUSOWA WOCHEZA NAYE: Kuyanjana ndi abale ndi alongo kumakuphunzitsani inu kuti munthu aliyense ali wosiyana ndi kuti wina afunikira kuphunzira kulemekeza kulingalira kwa ena. Chingakuthandizeninso pa sukulu, kuchipangitsa kukhala chosavuta kulongosola kwa ana ena. Koma ngati kuyanjana kwa kunyumba kusoweka, chotero yesani kukhala wofunitsitsa kufunafuna kwina kwake. Ngati sitero mudzakhala wosungulumwa. Inu mungadzimve kukhala wolekereredwa ndipo mwinamwake kungotsirizira kukhala wosungulumwa. Ichi chifunikira kupewedwa, monga mmene mfumu yanzeru yakale inachenjezera: “Wodzilekanitsa iyemwini adzafunafuna chifuniro chake chadyera; nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1, NW.

M’chenicheni, chotero, inu mungasankhe “abale” a inu eni ndi “alongo,” mogwirizana ndithudi ndi chivomerezo cha makolo. Al akuwona mu ichi zabwino zenizeni, akumati: “Ndimawona pa mabwenzi anga onse omwe ali ndi abale a makhalidwe oipa oterowo ndi alongo ndipo onse amadana wina ndi mnzake ndipo amamenyana nthaŵi zonse. Ndi mkhalidwe woipa chotani nanga.” Ndithudi, uwu suli mkhalidwe m’mabanja onse, koma iridi nkhani kaŵirikaŵiri ya kupangira nsonga yeniyeni.

Chifukwa cha kukhala ndi zochepa m’kuyanjana kwa panyumba, inu mungakhale ndi nthaŵi yambiri ya kuphunzira, kusinkhasinkha, kapena kukulitsa luso linalake. Ana ambiri obadwa okha apambana malingaliro akusungulumwa kapena kusowa woyanjana naye mwa kukhala woŵerenga wofunitsitsa. Chotero chiri mwinamwake osati chopanda chifukwa kuti mwana wobadwa yekha amawonedwa kaŵirikaŵiri monga mwana wochenjeretsa, wina amene mwachidziŵikire kwenikweni angakhoze kukulitsa mphamvu yaikulu ya kusunga mawu, mmodzi amene angakhoze kupambana m’zamaphunziro.

KUSAMALITSA KOCHULUKIRA: “Monga mwana wobadwa yekha ndinasonyezedwa kusamalira kotheratu ndi makolo anga,” anatero Thomas, ndipo amachilingalira icho kukhala mwaŵi. Ndithudi, kusamalitsa kopambanitsa kwa ukholo kungakhale koipa, kuwononga mwana, kum’pangitsa iye kukhala wodzitukumula. Kapena kungakhale kwa nkhalwe. Koma kumbali ina yabwino, ngati mumadzimva kuti makolo anu ali ndi nthaŵi yochepera kwenikweni kaamba ka inu—monga mmene ana ambiri amachitira—ganizirani mmene icho chikakhalira choipirapo ngati mukanafunikira kugawana nazo ndi abale osiyanasiyana ndi alongo. M’chenicheni, kusamalira kosagawanika kwa makolo anu kungakuthandizeni kukula mwamsanga, kudzimva wosungika pakati pa achikulire, ndipo kukhala wokhoza kukambitsirana ndi achikulire pamlingo wawo.

KUGWIRIZANITSIDWA KWA MAYANJANO: Chifukwa chimodzi cha kumvera chisoni kwa Sue Ann kaamba ka kukhala mwana wobadwa yekha chiri ichi: “Pamene muli nokha, mumakhala wopanda zogwirizanitsidwa. . . . Chiri chovuta kupeza wopita naye kocheza. Mukafunikira kupita ndi bwenzi lamwamuna la bwenzi la pamtima la bwenzi lanu lachikazi, kapena chirichonse. . . . Abale ndi amene ndikhumba kuti ndikanakhala nawo. Abale achikulire.” Komabe, mungakhale ndi nzeru kuyembekeza kufikira pamene mwakula mokwanira kuti mukwatire musanachite chibwenzi ndi mtsikana. Ndipo ngati ubwenzi ndi umene inu mufuna, kumbukirani kuti kugwirizanitsidwa kwa mayanjano kungapangidwenso kupyolera mwa mabwenzi. Kumbali ina, kusoweka kwa kugwirizanitsidwa kwa mayanjano ndi ziwalo za anthu okhala ndi ziwalo zogonanira zosiyana mkati mwa zaka zokongola za uchichepere sikuli moyenerera chinthu choipa. Mu kufuntha kwa masewera kwa lerolino, dziko lokhala ndi chilakolako chogonana choposerapo, iko kungakhaledi chinjirizo.

Lingalirani za Ena

Monga mwana wobadwa yekha, inu mungavomerezane ndi Jay, amene anati: “Chiri chabwino chifukwa chakuti sindimafunikira kugawana zovala, galimoto kapena chirichonse.” Icho chingakhale chabwino, koma m’kupita kwanthaŵi chingapangitse kaamba ka mtendere waukulu ngati muphunzira kugawana, ngakhale pamene inu simufunikira kutero. Zowona, inu mulibe abale kapena alongo amene mufunikira kugawana nawo, koma mwinamwake muli ndi asuweni kapena achibale ena. Motsimikizirika, inu muli ndi mabwenzi. Ndipo kodi cholakwika nchiyani mu kugawana ndi makolo anu?

Peter akuyamikira nthaŵi imene makolo ake anawononga kumuphunzitsa iye kugwira ntchito ndi manja ake: “Ndinapanga mphatso zambiri, za zinthu zamtundu uliwonse, ziri zonse zimene ndinazilingalira,” iye akutero, “ndipo ichi chinandiphunzitsa ine kuti ungapangitse ena kusangalala ndipo mwakutero kudzipangitsa iwemwini kukhala wosangalala kwenikweni kuposa onse.” Inde, mwambo wakuti “muli chimwemwe chambiri m’kupatsa kuposa ndi chimene chiri m’kulandira” udakafunikira kutsutsidwa.—Machitidwe 20:35.

Kulitsani diso la zosowa za ena. Kodi mungapatse winawake liwu lolimbikitsa? Kodi mungathandizire winawake yemwe ali wosowa mwa zinthu zakuthupi? Kodi mungapereke mauthenga kwa obindikiritsidwa kapena okalamba? Ngati muli mmodzi wa Mboni za Yehova, kodi mungagawane chidziŵitso cha Baibulo ndi ena kapena kuthandizira Akristu anzanu kupezeka pa misonkhano kapena kugawana mu kulalikira Kwachikristu?

Tsatirani Zitsanzo Zabwino

Baibulo limatchula munthu wachichepere amene anali “mwana mmodzi yekha.” Kodi mukudziŵa amene uyu anali? Tembenukirani ku Oweruza mutu 11 maversi 29 kufika ku 40, ndipo ŵerengani ponena za mwana wamkazi wa Yefita.

Mwana wamkazi wa Yefita mwachiwonekere sanali mwana wosungulumwa, popeza Baibulo likunena kuti anali ndi “mabwenzi achikazi.” Ndipo ndithudi, iye sanali woipitsidwa kapena mwana wodzikuza. Pamene anaitanidwa kuti akagwirizane ndi kufunika kwa chowinda cha atate wake, iye anali wofunitsitsa kuika zikondwerero za Mulungu patsogolo pa zilakolako za chibadwa zonga chikwati ndi kukhala mayi. Anthu achichepere ambiri lerolino akutsatira chitsogozo chake.

Tengani Thorsten, mwachitsanzo, amene tsopano akutumikira monga minisitala wa nthaŵi zonse mu nthambi ya ofesi ya Watch Tower Society mu Europe. Iye akuti: “Ngati ndikanakhala ndi abale ndi alongo, ine mwachiwonekere sindikanakhoza kukumana ndi mavuto ena. Kumbali ina, sindikanakhoza kukumana ndi maora achisangalalo ochulukira amene ndinali wokhoza kuwononga ndi mabukhu anga, ndipo mwinamwake sindikanakhoza kukulitsa chiyamikiro chathithithi kaamba ka chowonadi, kaamba ka ubale, ndipo kaamba ka utumiki chimene tsopano ndiri nacho. Ndimafunabe kukhala ndekha panthaŵi zina. Koma sindiri wosungulumwa chifukwa chakuti ndaphunzira kudzisunga inemwini kukhala wotanganitsidwa. Sindirinso mwana wobadwa yekha—chifupifupi osati motheratu tero.”

Inu, nanunso, monga mwana wamkazi wa Yefita ndipo monga Thorsten, mungapeze chisangalalo monga mwana wobadwa yekha.

[Chithunzi patsamba 20]

Ine kaŵirikaŵiri ndimasowa kaamba ka kukhala wopanda mlongo; komabe ndiri ndi zabwino zina

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena