Tsamba 2
Mkati mwa zaka mazana, mamiliyoni amapemphero akhala akunenedwa kaamba ka mtendere.
Mwinamwake palibe lirilonse limene limakhala lachilendo mofanana ndi awo operekedwa ndi atsogoleri a chipembedzo a dziko lonse pa Asisi, Italy, kumapeto kwa 1986.
Nchiyani chimene chinachitika kumeneko? Kodi msonkhano umenewu unali wowonekera? Kodi anthu a zipembedzo zimenezo anamvetsera ndi kuchita mogwirizana ndi mapempherowo? Kodi Mulungu anamvetsera?
Wolemba Galamukani! mu Italy akundandalitsa mafunso amenewo m’nkhani zotsatirazi.