Ntchito Zachifundo Zimabweretsa Chisangalalo
Sikale kwambiri pamene kalata yotsatirayi inalandiridwa ndi afalitsi a Nsanja ya Olonda:
“Bwana Wokondedwa:
“Mwezi watha mu Philadelphia mwana wanga wamkazi wa zaka za pakati pa 13 ndi 19 anaberedwa chikwama chake chandalama muphukusi la thumba la mabukhu. Mlungu wathawu, mu m’tokoma analandiriramo phukusi limene linali ndi chikwama chake chandalama ndi laisensi ndi makardi ena ofunika. Phukusilo linatumizidwa ndi munthu wina amene sanafune kuti adziŵike, kusiyapo kokha kuti phukusilo linalinso ndi kope la magazini anu a Nsanja ya Olonda. Aliyense amene anasonyeza chikondi chaubale ichi (kuchokera ku mzinda wa chikondi chaubale) iye anadzivutitsa mu kuwononga ndalama yake kuchibwezera kwa mwana wanga wamkaziyo. Banja langa likuyamikira kwambiri kwa munthu wachifundo uyu . . . inali njira yabwino kwambiri ‘kuchitira umboni, makamaka kwa a zaka za pakati pa 13 ndi 19 anga (3 a iwo).”
Kuŵerenga Nsanja ya Olonda kwayambukira mopindulitsa miyoyo ya mamiliyoni, kukulitsa mwa iwo mikhalidwe ya kuwona mtima, chifundo, ndi kukoma mtima. Tsopano makope oposa mamiliyoni 12 a chotuluka chirichonse amasindikizidwa mu zinenero zoposa 100. Inu mungalandire kulembetsa kwa Nsanja ya Olonda, makope aŵiri pa mwezi mwakungolemba ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi K32.00.
Chonde tumizani Nsanja ya Olonda. Ndatsekeramo K32.00.