“Ndidyeni Ngati Mulibe Mantha!”
Ngakhale ngati kachirombo kalibe mantha, sichikakhala chopepuka. Atakwiyitsidwa, mapufferfish amakulitsa thupi lawo kukhala monga mpira wozungulira. Samapangitsa kuwameza kukhala kopepuka. Ndiponso, pamene zadzifufumitsa izo zeni, zikwi za zisonga zakuthwa za zibowo zimatuluka mu mibowo ya khungu lawo. Kumeza thupi lokhala ndi zinthu zakuthwa zoterozo kumapangitsa m’mero wokandika kwambiri.
Ngati zonsezi siziri zokwanira kuletsa mdani ndipo mwakutero apambana kumeza puffer, mavuto ake ndithudi amayamba. Nsomba za puffer ziri zodzaza ndi ululu woipa. Ululu woipa uli umodzi wa ululu wa nyama za m’madzi wodziŵika bwino koposa.
Mosasamala kanthu za ichi, nyama yake imaikidwa pamwamba kwambiri ndi anthu a Kum’mawa. Yotchedwa fugu ndi anthu a ku Japan, iyo imadyedwa ngakhale yosaphika monga sashimi. Imapha anthu ambiri chaka chirichonse. Bukhu lakuti Undersea Life lalongosola kuti:
“Mosasamala kanthu za kuwopsya, okonda fugu amasangalalabe ndi kudzimva kwa chisangalalo chochepa, kutentha ndi kuzizira kwa mwazi, ndi kudzimva kwa kudzidzimuka kochititsidwa ndi mankhwala ‘olamulidwa’ a ululuwo, kuphatikizaponso ndi kukoma kosakhala kwanthaŵi zonse kwa nyama. Popeza ngakhale zizindikiro za kupha kwa ululu woipa zimaphatikizapo kuchita thukuta, kumva mutu kuwawa, nselu, kufa kwa ziwalo zopumira, zironda za m’thupi, kutulutsa mwazi, kulefuka kwakukulu popanda kukomoka, ndipo nthaŵi zina kufa kotheratu kwa mphamvu zonse, chiri chodabwitsa kuti okonda sashimi samamatira ku nsomba za tuna ndi sea bass.”—Tsamba 180.