Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 11/8 tsamba 29-30
  • Kumaliyang’ana Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumaliyang’ana Dziko
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mavideo Oipa
  • Chinjirizo la Mtengo Wapamwamba
  • Kuchiritsa Kwatsopano kwa Chimfine?
  • Kulambira Kwachindunji
  • Makardi Achipulumutso
  • Kubera Boma
  • Kulira Kosiyana
  • Asilikari Okalamba ndi Nkhondo ya pa TV
  • Kusowa Tulo Kosatha
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Akhristu Ayenera Kumapemphera mu Akachisi?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Zimene Mungachite Kuti Muzigona Bwino
    Galamukani!—2003
Galamukani!—1987
g87 11/8 tsamba 29-30

Kumaliyang’ana Dziko

Mavideo Oipa

Chipatala chotsegula mitima m’chimene odwala amafa ndi nthenda ya mtima, kuphedwa kwa oukira boma mwa kuwalizira mfuti, ogwidwa ndi mlandu akufa mu mpando wa magetsi, ndi kukhadzulidwa kwa mlonda wosunga mokhala nyama kufikira imfa ndi ng’azi ziri kokha ziwonetsero zenizeni za imfa zomwe tsopano ziripo kaamba ka kupenyereredwa pa makaseti a mavideo olipiritsa. Mpambo wa kuwonetsa kutatu wotchedwa Faces of Death umasonyeza kuvumbulutsa kowawa kwa zithunzithunzi zenizeni za anthu akufa. Kodi kuyankha kwa anthu nkotani ku mpambo umenewu wa mavideo? “Sitingawalekerere iwo,” kalaliki mmodzi wa sitolo la mavideo mu Virginia Beach, Virginia, anauza The Virginian-Pilot and the Ledger-Star, magazini ya ku Virginia. “Mwamsanga itayambika, winawake amaifufuza.” Wopenyerera wokwiyitsidwa mmodzi mwa kutsutsa ku ziwonetsero za kanemayo wayambitsa ndawala ya kupangitsa masitolo a kumaloko kuchotsa mavideo. Akumalongosola za kanemayo, iye anati: “Iyo iri mwachiwawa yonyansa.”

Chinjirizo la Mtengo Wapamwamba

Ndi kubedwa kwa zinthu kwa mtengo wapamwamba mu eni masitolo a mu United States kwa chifupifupi $30 biliyoni pa chaka, chiri chosadabwitsa kuti pali indastri yomakula yomwe imatulutsa ziwiya zoletsera kuba zinthu m’masitolo. Pakati pa izi pali EAS (Electronic Article Surveillance) Zopangidwa zotchedwa targets. Izo ziri monga timapulasitiki tosalala tomwe timaikidwa ku zinthu zonga ngati zovala, nthambo za magnet “zazing’ono monga tsitsi la munthu,” kapena “magwero a magetsi omwe apangidwira mkati mwa chiwiya cha mtengo chowonekera.” “Matargets” angachotsedwe kapena kuletsedwa kugwira ntchito ndi anthu ogwira ntchito panthaŵi imene inu mulipira zinthu zomwe mwagula. Anthu ogula m’masitolo omwe amagwiritsira ntchito zinthu zimenezi amafunikira kutuluka kapena kupyola pambali pa magwero amene amapereka zizindikiro ngati “target” silinaletsedwe kugwira ntchito bwino. Kugulitsidwa kwa zinthu izi kwafika kale pa $150 miliyoni.

Kuchiritsa Kwatsopano kwa Chimfine?

Nchifukwa ninji chimanenedwa kuti odula mitengo a ku Norway samayambukiridwa ndi chimfine? Malingana ndi Dr. Olav Braenden, yankho liri kaamba ka utsi wa nkhuni womwe amapuma, inasimba motero The Times ya ku London. Kachirombo ka chimfine kamafunikira kuperekedwa kwabwino kwa mpweya womwe tipuma kuti kabale. Komabe, iko kangaletsedwe ndi mavitamini B ndi C ndiponso, chikukhulupiriridwa kuti, ndi polyphenols. Zinthu zimenezi, zomwe zimapezeka mu utsi wa nkhuni za ku Norway, zimachepetsako kutengedwa kwa mpweya womwe tipuma pa mtsempha wa m’mphuno wa mamina. Chasimbidwa kuti madontho otuluka m’mphuno okhala ndi zinthu ziŵirizi ayesedwa pa malo a anthu 300 ogwira ntchito mu gulu lankhondo la mlengalenga a ku Norway ndi kukhala ndi mlingo wa kuchiritsa kopita patsogolo kwa chimfine kwa maperesenti 82. “Chinthu chofunika chiri kutenga madonthowo pa zizindikiro zoyamba za chimfine,” wagogomezera motero woyang’anira wa kufufuzako Dr. Anton Rodahl, “pamene kachiromboko kasanapange kuvulaza kulikonse ku epithelium [khungu la mkati] m’mphuno.” Zogulitsidwa za malonda zamankhwalawo zinayambika mu Norway chaka chino.

Kulambira Kwachindunji

Ana a sukulu a ku Japan, odera nkhaŵa ndi kulowa sukulu, amagwiritsira ntchito nzeru za zopangapanga kufikira chonulirapo chawo. Amachita tero motani? Kulingana ndi Asahi Shimbun, nyuzipepala ya ku Tokyo, wophunzira amalowetsa dzina lake, keyala, chaka cha sukulu, ndi dzina la sukulu loyembekezeredwa mu magwero achindunji olumikizidwa ku telefoni. Ndiyeno chidziŵitso chimenechi chimaperekedwa ku malo opatulika a Shinto kumene wansembe amachiŵerenga ndi kupereka mapemphero pa chopereka cha 3,000 yen ($20, U.S.). Maulamuliro a malo opatulika anena kuti, “Kulambira pa guwa inumwini ndithudi kuli kofunika.” Komabe, wansembe wa ku Dazaifu Tenmangu mu Kyushu, malo opatulika ofala kwambiri mu Japan operekedwa ku maphunziro, analongosola kuti anthu ochenjera okhala kufupi ndi malo opatulika akhala akulipiritsa kufika ku 20,000 yen ($140, U.S.) kaamba ka kuimira olambirawo. Ansembe anatsutsa kaamba ka kupangidwa kwa kulambiraku kukhala malonda ndi anthu omwe sanali ogwirizana ndi malo opatulika. Iwo analingalira kuti: “Uchindunji umaperekanso malingaliro amtima. Ziyambukiro ziri zimodzimodzi,” ndipo anapereka mautumiki pa mtengo wochepa.

Makardi Achipulumutso

Nkhole za anthu akufa kaamba ka kugwa chakhala chodera nkhaŵa cha nthaŵi yaitali cha anthu otsetsereka pamwamba pa madzi ndi mapiri mofanana. Ngakhale kuti mitundu yosiyanasiyana ya zolandirira mawu ziripo, anthu ochepa amazigwiritsira ntchito izo chifukwa cha mtengo wake ndi mlingo wa kulema ndi kukula kwa zokhala ndi mphamvu za mabatili zina. Komabe, gulu la ofufuza a chiFrench akugwirira ntchito pa lingaliro latsopano—makardi achipulumutso. Okhoza kunyamulidwa pa chifuwa ndi kumbuyo kwa wotsetsereka aliyense kapena okwera mapiri, zingakhoze kokha kugulidwa ndi madola ochepa, zosafunikira mabatili, ndipo zingakhale chifupifupi mlingo wa kardi ya ngongole. Kodi zimagwira ntchito motani? Nyuzipepala ya tsiku ndi tsiku ya chiFrench Le Figaro yachitira ripoti kuti izo zingagwire ntchito monga akalilole, mwakutumiza mbali ya zizindikiro za radio kwa gulu lopulumutsa lokonzekeretsedwa ndi zolandirira zamphamvu ndithu. Mu kufufuza kochitidwa ndi zofufuzira, ofufuza apambana kale m’kupeza anthu oikidwa pansi pamadzi owumbana ochulukira ndi mapazi 30 (9 m).

Kubera Boma

Kuŵerengera kwaposachedwapa kwa chuma cha mu Canada kunavumbula zowonongedwa zochokera pa $3 miliyoni kufika ku $4 miliyoni mu chuma cha dziko pachaka. Ngakhale kuti zinthuzo zalongosoledwa mwalamulo kukhala zikusowa, chinavomerezedwa kuti izo “mwinamwake zinabedwa.” The Toronto Star inasimba kuti pakati pa zinthu zosowa pali zakumwa, TV yosonyeza mitundu, mataipi, nyali za pa desiki, dictaphones, 35-mm cameras, overhead projectors, zopendera, denga la motor, ndi choziziritsa zakudya. Mtundu wina wa kuba kuchokera ku boma unasonyeza kuchulukira kwapamwamba kwa chifupifupi $60 miliyoni yotengedwa kuchokera ku ndalama zosungidwa kaamba ka osapeza ntchito a ku Canada ndi anthu omwe anayesa kuchotsapo dongosolo limenelo. “Panali zochitika 180,458 za kunyenga,” kulingana ndi nyuzipepala ya The Globe and Mail. Mwachisangalalo, pa zowonongedwazo, “$32.3 miliyoni inapezedwa.”

Kulira Kosiyana

Kodi mayi angazindikire kulira kwa khanda lake kuchokera ku kuja kwa ena? Inde, inasimba tero The Sunday Times ya ku London. Koma kuzindikira kwa mayi kumapita ngakhale kuposa apo, kulingana ndi zopezedwa za Dr. Alain Lazartigues, dokotala wa maganizo wa ana pa chipatala cha La Pitié Salpetrière mu Paris. Kuchokera ku phokoso la kulira, iye angakhozenso kuzindikira chifukwa cha kuchitira tero, ngati mwanayo ali ndi njala, kunyowa, kukalipa kapena kudwala. Njala, chochititsa chofala cha kulira kwa khanda, kuli ndi phokoso la kulira kwapamwamba kwa pakati pa 270 ndi 450 hertz ndipo kumakhala pakati pa 80 ndi 85 decibels. Kulira kwa kuwawa, kukalipa, kuyambukiridwa, ndi kwa chisangalalo, dokotalayo wanena kuti, nakonso kuli ndi kudziŵika kwake kwapadera. Iye wadziŵitsa kuti kwa matenda ena ake, kulira kwa mwana kungatsimikizire kukhala kwa thandizo mu kufuna kudziŵa zizindikiro.

Asilikari Okalamba ndi Nkhondo ya pa TV

Chiwawa ndi nkhondo zimasonyezedwa mokhazikika pa wailesi ya kanema ndi maprogramu a nkhani. Makamaka, akanema, amawonekera kusonyeza mkhalidwe wa nkhondo mu njira yolemekezeka. Asilikari ankhondo okalamba, ngakhale kuli tero, omwe akumana ndi kuwawa kwake koipa kaŵirikaŵiri amalephera kupeza chosangalatsa cha zochitika zoterozo za pa wailesi ya kanema. Stan Knorth, msilikari wokalamba wa Nkhondo ya Dziko I, yemwe tsopano ali ndi zaka zakubadwa 90, anawuza St. Louis Magazine: “Ndikawona kuliziridwa mfuti konseko ndi zonyansa pa TV, ndimaitseka.” Chifukwa chake? “Sindingakhoze kuchita nalo. Sindifuna kuikumbukira iyo,” analongosola tero Knorth.

Kusowa Tulo Kosatha

Munthu wodwala kusowa tulo kosatha anakhala miyezi isanu ndi inayi popanda kugona ndiyeno pambuyo pake anafa, inasimba tero Evening Press ya ku Dublin, Ireland. Akumalongosola chochititsa imfa, Profresala Elio Lugaresi, katswiri wodziŵa za bongo wa pa University of Bologna Medical School mu Italy, analongosola kuti nthenda yosachitika kaŵirikaŵiriyo imayambukira thalamus, magwero a mtsempha wa mbali ya bongo womwe umapititsa uthenga pakati pa bongo ndi thupi. Pamene kukambitsirana kunasokonezeka, “malo apakati a bongo anagwira ntchito monga motor imene sikanakhoza kuimitsidwa.” Ngakhale kuti wodwalayo anayesa kulimbana ndi matendawo, iye anadzakhala chiwalo cha 14 cha banja lake chomwe chinafa, chiyambire 1822, kaamba ka kusoweka kwa kugona. Ripoti la Lugaresi pankhaniyo lagalamutsa asayansi ena kudziŵa mbali yaikulu imene zoyambukira mitsempha kuchokera kwa makolo ndi mbali ya bongo zimachita mu nkhani ya kusowa tulo. Lugaresi akulongosola kuti: “Timadziŵa kugwira ntchito kwa matendawo, koma tiribe njira iriyonse ya kuwaletsera.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena