“Chitetezero cha Thanzi Langa”
Ndizo zimene wolembetsa wina wa ku Senegal, West Africa, adanena za magazini ya Galamukani! Iye analemba kuti:
“Ndiri wosangalala kwambiri kuti ndimaŵerenga Galamukani! nthaŵi zonse chifukwa cha nkhani zabwino kwambiri zimene imasimba. Zoyenerera ndendende ndipo zofunika kwambiri kaamba ka tsiku lathu lamakono. Ndine wolembetsa kwa zaka ziŵiri ndi theka. Kudzera m’kalatayi ndikufuna kuyamikira alembi ndi ofalitsa kaamba ka thandizo lawo ku chitetezero cha thanzi langa, ndipo osati langa lokha komanso la ena ambiri omwe akhala okhoza kuleka zizoloŵezi za fodya ndi kutetezera thanzi la iwo eni mwakupeza nyonga yofunika kudzera m’kuŵerenga nkhani za mu Galamukani! Chonde pitirizani kukonzekera nkhani zonena za maupandu a fodya, popeza kuti ndikupeza kuti mbali zitatu za zinayi za achichepere amene ndimakhala nawo amasuta fodya, imene iri yaupandu osati ku thanzi lawo lokha ndi la ena komanso kuwononga ndalama zawo. Ndiyamikira kaamba ka zonse zimene ndimapeza poŵerenga magazini anu.”
Tiganiza kuti inu, nanunso, mudzapindula mwakuŵerenga Galamukani! Landirani kulembetsa kwa chaka chimodzi mwakungolemba ndi kutumiza kapepala kotsatirapoka limodzi ndi K16.00 yokha.
Chonde tumizani kulembetsa kwa chaka chimodzi kwa Galamukani! Ndatsekeramo K16.00 kaamba ka makope 12 a magazini imeneyi (kope imodzi pa mwezi).