Tsamba 2
Makolo mamiliyoni angapo kuzungulira dziko lonse ataikiridwapo mwana. Matenda, njala, nkhondo, kuphedwa, kudzipha, ngozi, imfa ya mwangozi, kupita padera, kubala mwana wakufa—mosasamala kanthu ndi chomwe chingakhala chochititsa, kholo nthaŵi zonse limakhala ndi chisoni.
Mosasamala kanthu za msinkhu wa mwana, kuŵaŵa nthaŵi zonse kumakhalapo. Kodi chisonicho chingapiriridwe motani? Kodi ndimotani mmene moyo ungapitirizirebe? Kodi chisonyezero chathu patsambali cha banja likulandiranso mwana wawo kuchokera kwa akufa chiri kokha loto, kapena kodi icho posachedwapa chidzakhala chenicheni?
Nkhani zowona zotsatirazi za anthu omwe apulumuka chisoni chowopsya chochititsidwa ndi kutaikiridwa kwa mwana zidzayankha ena a mafunso ameneŵa. Kaamba ka zotulukapo mu chimodzi ndi chimodzi cha izo, chonde ŵerengani nkhanizi za chisoni. Tikhulupirira kuti mudzapeza chitonthozo ndi chiyembekezo kuchokera mu izo.