Nchiyani Chimene Mboni za Yehova Zimakhulupirira?
Atsogoleri a m’midzi mu Roma wa zana loyamba anauza mtumwi Wachikristu Paulo kuti: “Tikufuna kumva zimene mukhulupirira, pakuti chinthu chokha chimene tidziŵa ponena za Akristu amenewa chiri chakuti awanenera ponse ponse!” (Machitidwe 28:22, The Living Bible) Anthu amenewo anafuna kumva kuchokera ku magwero m’malo mwa osuliza akunja okha.
Lerolino, Mboni za Yehova zimaneneredwa moipa kaŵirikaŵiri, ndipo chikakhala kulakwa kuyembekezera kuphunzira chowonadi ponena za iwo kuchokera ku magwero osuliza. Chotero tiri osangalatsidwa kugaŵira mabroshuwa atatu a masamba 32 amene amalongosola zikhulupiriro za Mboni za Yehova, otchedwa Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century, School and Jehovah’s Witnesses, ndi Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi, kokha pa K7.20.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, mabroshuwa atatu Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century, School and Jehovah’s Witnesses, ndi Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuno cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi. Ndatsekeramo K7.20.