Kumaliyang’ana Dziko
AIDS Iwopsyeza Asia
Nthenda yakupha ya AIDS ikuwopsyeza Aisa ndi mliri, inachenjeza tero WHO (World Health Organization). “Ngati tilola AIDS kufalikira mu Asia, ndiko kuti tidzakhala ndi vuto kwenikweni,” anatero mtsogoleri wa zaumoyo wa WHO Halfdan Mahler, kulingana ndi gulu lofalitsa nkhani ya mitundu yonse. Ngakhale kuti North ndi South America tsopano ziri ndi chiŵerengero chapamwamba cha matenda ochitiridwa ripoti a AIDS ndipo Asia chaching’ono, WHO ikuwopa kuti pamene kachirombo kodzetsa imfa kafalikira ku mitundu yokhala ndi chiŵerengero chokulira cha anthu ku Asia, boma silidzakhala lokhoza kufufuza kakulidwe kake. “Ndiri ndi mantha kuti muli ndi malo kaamba ka tsoka lokulira,” anatero Mahler. “Ndiridi ndi mantha ponena za chimenecho.”
“Malonda a Anyani”
Ngati munali m’malonda a coconut, kodi ndani yemwe mukalemba ntchito monga wotola? Mu dera la kumpoto la Surati Thani, Thailand, kampani imodzi inalowetsa ntchito chifupifupi anyani 800 kuchita ntchitoyo. Pansi pa mphatso ya $4,000 (U.S.) yoperekedwa ndi banja lachifumu la ku Thai, anyani akupatsidwa chiphunzitso chaluso cha mmene angatolere macoconuts m’mitengo. Komabe, “palibe nyani wachikulire aliyense yemwe angachite chimenecho,” inachitira ripoti tero The Economist. Ena alibe chifuno kaamba ka ntchito, monga mmene ziriri zowona ndi ‘okhala ndi nsidze zoyera’ kusiyanasiyana kwawo—iwo kaŵirikaŵiri amatsimikizira kukhala aulesi kwambiri. Mosiyanako, nyani wokhala ndi chizoloŵezi cha ntchito angakhoze kutola unyinji wa macoconut zikwi zingapo tsiku lirilonse, inadziŵitsa tero The Economist. Ngati akanapatsidwa malipiro olingana ndi ntchito yake, iye akapeza kuposa mtumiki wa boma wapakati mu boma la Thai. Mosasamala kanthu ndi umoyo wa ntchito wa kokha chifupifupi zaka zisanu, iwo ali oyenerera bwino lomwe kukhala chuma chosungidwa. Iwo amawononga chifupifupi $40 kuti aphunzitsidwe.
Akazi Amakhala ndi Moyo Wotalikirako
Chakhala chikudziŵika kwa nthaŵi yaitali kuti akazi amakhala kwa nthaŵi yaitali kuposa amuna. Kufufuza kwa posachedwapa kwasonyeza kuti, ngakhale mu umoyo wa kubadwa kusanachitike, imfa za m’mimba, pa avereji, zakhala zochulukira 50 peresenti pakati pa makanda osabadwa achimuna kuposa pakati pa makanda osabadwa achikazi. Tsopano, nkhani yofalitsidwa mu British Medical Journal yatsimikizira kuti akazi amakhalabe kwa nthaŵi yaitali kuposa amuna. Alan Silman, mkonzi wa nkhaniyo ndi mphunzitsi pa London Hospital Medical College, wadziŵitsa kuti ngakhale m’maiko otukuka kumene, akazi amachitira avereji zaka chifupifupi zisanu ndi chimodzi zowonjezereka za kuyembekezeredwa kwa umoyo kuposa mmene amuna amachitira. Iye akusimba kuti mu England ndi Wales, gulu lachitatu la chiŵerengero chonse cha akazi a zaka 65 angayembekeze kupulumuka ku msinkhu wa zaka 80, kulinganizidwa ndi kokha aŵiri mu amuna asanu. Chochititsa? Akazi ali ndi chizoloŵezi cha kukhala ndi ngozi zochepera, amachezera adokotala awo kaŵirikaŵiri, ndipo mwinamwake chofunika koposa, amasuta mochepera. Kuwonjezerapo, uchidakwa uli wosafala pakati pa akazi kuposa pakati pa amuna. Komabe, kulingana ndi Mr. Silman, “pali kuwawa kobisika.” Zaka zowonjezereka zimene akazi amapulumuka ziri kaŵirikaŵiri za “mkhalidwe woipa,” zotsirizidwa mu kudzipatula kwa mayanjano ndi kusauka.
Opanda Nyumba Kulikonse
Munthu wachinayi aliyense padziko ali kaya wopanda nyumba kapena amakhala pansi pa “makoma owonongeka ndi a mkhalidwe wosakhala waumoyo wabwino.” Kufufuza kochitidwa ndi Mitundu Yogwirizana kunavumbula kuti chifupifupi anthu mamiliyoni 100 anakhoza kugona m’makwalala, pansi pa maulalo, m’zipata, kapena pa malo osiidwa. Maperesenti makumi aŵiri a anthu oterewa ali achichepere mu Latin America. Mu mizinda ya mu Africa, kufika ku maperesenti 80 a nzika zonse amakhala m’nyumba zauve. United States iri ndi anthu opanda nyumba mamiliyoni 2.5, ndipo mu Great Britain chiŵerengero chiri chifupifupi 250,000.