Tsamba 2
“MWACHISAWAWA nthaŵi yokha pamene njovu imatenga kaimidweka [makutu atatambasulidwa] iri pamene yawopsezedwa ndipo iri pafupi kubangula.”—Cynthia Moss, mu “Portraits in the Wild.”
Irinso nthaŵi kaamba ka chinthu chomwe chachititsa kudera nkhaŵa kwake kukhala chowopsyedwa—matani asanu ndi aŵiri a mkwiyo akumadzetsa chiwunda kwa inu alidi pafupi.
Koma munthu ali chiwopsyezo chachikulu cha njovu kuposa mmene njovu iliri kwa munthu. Mtengo wa m’nyanga wakwera kwambiri, zazimuna zazikulu zimanyamula oposa mapaundi 400 (180 kg) a iyo, ndipo malamulo samaletsa akupha nyama popanda lamulo. Iwo amatenga nyangayo ndi kusiya zotsalazo kuti ziwole. Chiri choipa chotani nanga. Chiri chomvetsa chisoni chotani nanga.