Madzi Otentha a Kumpopi Angakhale Odzetsa Ngozi ku Umoyo
“KUSAMBA madzi otentha, kuchapa zovala za banja kapena kutsuka mbale za chakudya cha masana kungakhale kodzetsa ngozi ku umoyo wanu, kulingana ndi maphunziro omwe asonyeza kuti mlingo wapadera wa mankhwala odzetsa kansa umachokera ku madzi osungidwa m’nyumba mkati mwa kuwagwiritsira ntchito kwa tsiku ndi tsiku. Kuwunikiridwa ku trichloroethylene (TCE), zoipitsa zofala za madzi a pansi pa nthaka, ndi mankhwala akupha tizirombo ta m’madzi, chotulukapo cha msanganizo wa mankhwala akupha tizirombo, kungakhale kwapamwamba kuwirikiza nthaŵi 50 kuchokera ku kupuma nthunzi wa madzi koposa kumwa madzi, akutero wodziŵa za mankhwala Julian Andelman wa ku Yuniversite ya Pittsburgh Graduate School of Public Health. Maphunziro ake asonyeza kuti madzi a kumpopi otentha, mwachitsanzo, amatulutsa chifupifupi 50 peresenti ya mankhwala akupha tizirombo tam’madzi osungunuka ndi 80 peresenti ya TCE yosungunuka m’mpweya. Kwa anthu omwe amawononga nthaŵi yawo yochulukira panyumba, nthunzi wa madzi wochokera ku makina ochapira ndi makina otsukira mbale ungakhoze ngakhale kukhala magwero a akulu akuwunikiridwa, akutero Andelman. Chenjezo: gwiritsirani ntchito madzi a kumpopi ndi kusamba kwanthaŵi yochepera, gwiritsirani ntchito madzi ozizira ndi kugwiritsira ntchito ziwiya zotulutsira utsi wa madzi kumene kuli kothekera kuti mutulutsire kunja nthunzi wa madzi.—International Wildlife, January/February 1987.