Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 1/8 tsamba 27-29
  • Kodi Panyumba Panu Pali Poizoni Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Panyumba Panu Pali Poizoni Motani?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala Mwachikatikati
  • Makemikolo—Ndi Othandiza Kapena Owononga?
    Galamukani!—1999
  • Pali Makemikolo Ambiri Amene Anthu Apanga
    Galamukani!—1999
  • Mukadwala Chifukwa cha Mankhwala
    Galamukani!—2000
  • Mbali Yoipa ya Mankhwala a mu Maindastri
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 1/8 tsamba 27-29

Kodi Panyumba Panu Pali Poizoni Motani?

MALINGA ndi magazini a Scientific American, anthu oposa 3,000 a ku United States ndi Canada, anasonyeza kuti “nzika zambiri zimakhala m’malo amene muli poizoni . . . mkati mwenimweni mwa malo omwe iwo amaganiza kuti ndi abwino, monga m’nyumba zawo, m’maofesi ndi m’magalimoto.” Chimaipitsa mpweya m’nyumba ndi nthunzi ya zinthu monga zopangitsira m’nyumba kukhala mwaukhondo, mankhwala othamangitsira a gulugufe, zomangira nyumba, mafuta, zonunkhiritsira m’nyumba, mankhwala ophera majeremusi, ndiponso ngakhale mankhwala ochapira zovala ndi nsalu zokutira mipando zomwe zikupangidwa masiku ano.

“Chimfine cha mu mlengalenga,” ndi matenda amene akatswiri opita mu mlengalenga ankadwala m’mbuyomu kufikira pamene anazindikira kuti matendawo amabwera chifukwa cha utsi kapena “nthunzi.” Mumamva fungo la chinachake pamene muli m’galimoto yatsopano kapena mukuyenda m’sitolo pafupi ndi mashelufu a mankhwala oyeretsera m’nyumba, ngakhale kuti zimakhala m’zitini kapena m’mapepala. Choncho ngati nyumba yatsekedwa, mwina n’cholinga choti mufundeko kukamazizira, nthunzi ya makemikolo osiyanasiyana imathandizira kuti m’nyumba mukhale mpweya woipa kuposa mmene kunja kungakhalire.

Nyuzipepala ya ku Canada yakuti Medical Post inati ana ang’onoang’ono ndiwo ali pangozi kwambiri. Iwo amakhala moyandikana kwambiri ndi pansi kuposa akuluakulu; amapuma mofulumira kuposa akuluakulu; amathera 90 peresenti ya nthaŵi yawo m’nyumba ndipo popeza ziŵalo zawo zisanakhwime, matupi awo sachedwa kuwonongeka ndi poizoni. Iwo m’matupi mwawo mumalowa lead wokwana 40 peresenti, pamene akuluakulu m’matupi mwawo mumalowa 10 peresenti yokha.

Kukhala Mwachikatikati

Popeza kuti mbadwo uno wa anthu ndiwo ukukhala m’malo oipitsidwa ndi makemikolo ndipo palibe wina wofanana nawo, pali zambiri zomwe tichite kuphunzira ponena za ngozi yake, choncho a sayansi ali tcheru. Sikuti tikangogwiritsa ntchito makemikolo nthaŵi yomweyo basi tizida nkhaŵa kuti tidwala kansa kapena kuti tifa. Anthu ambiri amakhala bwino chifukwa chakuti Mlengi analenga matupi athu modabwitsa. (Salmo 139:14) Komabe ngati timakhala pafupi ndi makemikolo a poizoni tiyenera kuchenjera.

Buku lakuti Chemical Alert! linati “makemikolo ena ali ndi poizoni woopsa chifukwa amasokoneza mmene [thupi] limagwirira ntchito akumapangitsa zizindikiro za matenda zimene simungathe kuzilongosola koma kumangoti sindikupeza bwino basi.” Kuti tichepetse kukhudzidwa ndi makemikolo sipachita kufunika kusintha moyo umene timakhala koma chabe kungochepetsako pang’ono zimene timachita tsiku ndi tsiku. Chonde, onani mfundo zomwe zili m’bokosi patsamba 28. Zina mwa izo zingathe kukhala zothandiza kwa inu.

Kuwonjezera pakuti muyenera kukhala ochenjera pamene mukugwiritsa ntchito makemikolo, chinthu chinanso chothandiza n’chakuti tingachite bwino ngati sitikudera nkhaŵa kwambiri makamaka ponena za zinthu zimene sitingathe kuziongolera. Pa Miyambo 14:30, Baibulo limati “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.”

Komabe anthu ambiri amavutika ndipo amadwala, nthaŵi zina ngakhale matenda ofa nawo, chifukwa cha poizoni wa makemikolo.a Mofanana ndi anzawo mamiliyoni ambiri amene akuvutika chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana, amene akuvutika ndi matenda ochitika chifukwa cha makemikolo ali ndi zifukwa zoyenera zoyembekezera m’tsogolo, chifukwa posachedwapa dziko silidzakhala ndi poizoni amene amavulaza anthu okhalamo. Anthu okhala ndi malingaliro oipa pamodzi ndi malingaliro awowo, adzakhala chabe mbiri yakale, monga nkhani yomaliza m’nkhani zino isoyezere.

[Mawu a M’munsi]

a M’zaka za posachedwa chiŵerengero chomawonjezereka cha anthu akhala akuvutika ndi matenda ochitika chifukwa chokhudzidwa ndi makemikolo osiyanasiyana. Vuto limeneli tidzalilongosola m’magazini ya Galamukani! yam’tsogolo.

[Bokosi patsamba 28]

Kuti Nyumba Ikhale Yaukhondo ndi Yabwino

Kuti muchepetseko kukhudzidwa ndi poizoni kumafuna chabe kuti musintheko pang’ono moyo umene mumakhala. Pano pali mfundo zingapo zimene mwina mungazione kukhala zothandiza. (Kuti mumve zowonjezereka, zatsatanetsatane, kafufuzeni mu laibulale ya kwanu)

1. Yesetsani kusunga makemikolo amene amatulutsa nthunzi pa malo amene sangaipitse mpweya m’nyumba mwanu. Makemikolo amenewa ndi monga formaldehyde ndi ena omwe amauma mwamsanga ngakhale pamene sikunatenthe kwenikweni, monga penti, vanichi, zomatira, mankhwala ophera tizilombo, ndi mankhwala amadzimadzi oyeretsera m’nyumba. Mafuta omwe sachedwa kuuma amatulutsa nthunzi yoipa. Pagulu limeneli pali zinthu monga benzene, amene ngati wachuluka ndipo ngati ukupuma nthunzi yake kwa nthaŵi yaitali akuti amapangitsa kansa, kubala ana opunduka, ndi mavuto ena okhudza ziberekero.

2. Chipinda chizikhala choti mpweya uzilowa bwino, kuphatikizapo kosambira. Madzi akamauma amasiya makemikolo ena monga chlorine ngati analimo. Izi zimapangitsa kuti chlorine kapena chloroform awundane.

3. Muzipukuta mapazi anu pamene mukulowa m’nyumba. Mwambo umenewu ukhoza kuchepetsako lead pa kalipeti ndi chigawo chimodzi mwa zisanu, inatero Scientific American. Zimachepetsakonso mankhwala ophera tizilombo, amene ena mwa iwo amachepa mphamvu mwamsanga ngati ali padzuŵa koma akhoza kutenga zaka zambiri ngati ali pa kalipeti. Njira ina imene ili khalidwe m’mbali zina za dziko lapansi, ndilo kuvula nsapato. Chosesera m’nyumba chotchedwa vacuum cleaner, makamaka chomwe chimakhala ndi bulashi yomazungulira kunsi chikhozanso kuchotsa makemikolo omwe angaipitse kalipeti.

4. Ngati mwathira mankhwala ophera tizilombo m’nyumba, zidole muzisiye kunja pafupifupi kwa masabata aŵiri, ngakhale kuti mwina pachikuto chake angalembepo kuti m’nyumba mukhala muli bwino pakangotha maola ochepa kuchokera pomwe mwathira mankhwala. Posachedwa asayansi azindikira kuti mapulasitiki ena ndi thovu lomwe limakhala mkati mwa zidole limasunga mankhwala ophera tizilombo ngati chinkhupule. Poizoniyu amalowa m’matupi a ana kupyolera pa khungu ndi pakamwa.

5. Chepetsani kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo. Frank Graham, Jr, m’buku lake lakuti Since Silent Spring, analemba kuti mankhwala ophera tizilombo “ali ndi nthaŵi yake pa nyumba ngakhale kumunda, koma osatsa malonda apangitsa anthu m’midzi kukhulupirira kuti n’koyenera kusungiratu mankhwala ambiri.”

6. Penti yonse yothetheka yokhala ndi lead muyenera kuichotsa, ndi kupakapo penti yopanda lead. Osalola ana kumaseŵera pomwe pali penti yokhala ndi lead. Ngati muona kuti m’mapaipi muli lead, mukatsegula tapu ya madzi ozizira muwaleke atuluke kanthaŵi kufikira mutaona kuti madziwo asintha kutentha kwake ndipo madzi a pa tapu ya madzi otentha simuyenera kumwa—Environmental Poisons in Our Food.

[Chithunzi patsamba 29]

Ana aang’ono ndiwo ali pangozi kwambiri chifukwa cha makemikolo oipitsa m’nyumba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena