Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 4/8 tsamba 32
  • Wachichepere Atonthozedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wachichepere Atonthozedwa
  • Galamukani!—1988
Galamukani!—1988
g88 4/8 tsamba 32

Wachichepere Atonthozedwa

Mochedwa pa chirimwe china, Denise anadzakhala bwenzi la wochinjiriza moyo mnzake. Pamene bwenzili linali laling’ono amayi ake anafa. Ndipo posachedwapa anataikiridwa atate ake mu imfa. “Ndinamutumizira iye mphatso ya kulembetsa kwa miyezi isanu ndi umodzi kwa Galamukani!” Denise akulongosola tero. Miyezi yoŵerengeka pambuyo pake, Denise analandira kalata yotsatirayi kuchokera kwa bwenzi lake:

“Ndinaŵerenga makope oyambirira aŵiri a Galamukani! ndipo ziŵiri za nkhanizo zinandithandiza ine kwenikweni. Ina inkakamba pa mmene tingapezere chitonthozo pambuyo pa kutaikiridwa winawake wapafupi kwambiri ndipo ina yake inakamba panjira zomwe tingalakire kupsyinjika. Sindingakuuze ukulu umene izo zandithandizira ine. Kalatayo inagwira mawu a Afilipi 4:7, ‘Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.’ Kuŵerenga chimenecho mwamsanga kunandipatsa ine chiyembekezo chatsopano. Ndikuyamikira kwambiri kaamba ka kundilembetsera ine Galamukani!”

Kodi mukudziŵa winawake amene angapindule kuchokera ku magazini ya Galamukani!? Nchifukwa ninji osamutumizira iye mphatso ya kulembetsa? Inu mungachite chimenecho mwa kungodzaza ndi kutitumizira kapepala, mukumatsekeramo K16.00 ndi kapepalako.

Chonde, tumizani mphatso ya kulembetsa ya chaka chimodzi ya Galamukani! kwa munthu wotsatirayu, kuphatikizapo kalata yolongosola kuti iyo iri mphatso yochokera kwa‐‐‐‐‐‐‐‐(dzina lanu). Ndatsekeramo K16.00.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena