Tsamba 2
Mowonadi mbadwo uliwonse watulutsa zoneneratu zake za kuyandikira kwa kutha kwa dziko.
Chotero, kodi chimenecho chimatanthauza, kuti palibe maziko kaamba ka zimene Mboni za Yehova zakhala zikulengeza chiyambire 1914—mapeto ku dongosolo iri la dziko la kachitidwe ka zinthu ndi dongosolo la dziko latsopano likudzalo lomwe lidzasintha dziko lapansi kukhala paradaiso? Kodi zonsezo ziri kokha mchitidwe wa kusalongosola bwino? Ku mbali ina, ngati Mboni za Yehova ziri zolondola, kodi chimenecho chidzakuyambukirani motani?
Mayankho ku mafunso onsewa ali ofunika kwenikweni kwa tonsefe, makamaka tsopano pamene tikukhala m’nyengo yapadera ya m’mbiri, mbadwo wa nyukliya, mmene munthu kwa nthaŵi yoyamba angapange ndemanga yakuti, “Sikungadzakhale ana aliwonse kapena zidzukulu.”