Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 5/8 tsamba 13-16
  • Masiku Otsiriza—Kodi Chotsatira Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masiku Otsiriza—Kodi Chotsatira Nchiyani?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mbadwo Ungakhaleko kwa Utali Wotani?
  • “Mtendere ndi Chisungiko” Posachedwapa?
  • Kachitidwe Kosankha ka Wokwera pa Kavalo Woyera
  • Nthaŵi ya Kudikira
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 5/8 tsamba 13-16

Masiku Otsiriza—Kodi Chotsatira Nchiyani?

“Ndikukuuzani chowonadi, mbadwo uno ndithudi sudzapita kufikira zinthu zonse zimenezi zitachitika.”—Yesu Kristu, Mateyu 24:34, New International Version.

YESU, pamene anali kulongosola “chizindikiro . . . cha kutha kwa dongosolo la kachitidwe ka zinthu,” ananena kwa ophunzira ake ozizwitsidwawo mawu omwe agwidwa pamwambapo. (Mateyu 24:3) Tsopano kodi nchiyani kokha chimene Yesu anatanthauza ndi liwu lakuti “mbadwo”? Ndipo kodi ndi zochitika zotani zimene zikatsogolera ku mapeto a dongosolo la zinthu? M’mawu ena, ndi zochitika zotani zimene tifunikira kuyembekezera mtsogolo mosachedwa?

Kodi Mbadwo Ungakhaleko kwa Utali Wotani?

The American Legion Magazine inalozera kuti amuna ndi akazi 4,743,826 a ku U.S. anagawanamo mu Nkhondo ya Dziko I. Koma mu 1984 kokha 272,000 anakhalabe ndi moyo, ndipo ankafa pa avereji ya asanu ndi anayi ora lirilonse. Kodi chimenecho kenaka, chimatanthauza kuti, mbadwo wa 1914 watha kale?

Liwu la Chigriki kaamba ka mbadwo liri geneá, logwiritsiridwa ntchito ndi Mateyu, Marko, ndi Luka mu zolembera zawo za mawu a Yesu. Ilo lingakhale ndi kugwiritsiridwa ntchito kosiyanasiyana kulingana ndi mawu a mkati. Komabe, The New International Dictionary of New Testament Theology imamasulira ilo monga: “Awo obadwa pa nthaŵi imodzi . . . Logwirizana ndi ichi liri tanthauzo: unyinji wa mabwenzi a wina, mwamsinkhu.” A Greek-English Lexicon of the New Testament yalongosola kuti: “Unyinji wa chionkhetso chonse pamodzi wa awo obadwa pa nthaŵi imodzi, chokulitsidwa kuphatikiza aja onse okhala pa nthaŵi yopatsidwa ya mbadwo, mabwenzi.” Matanthauzo amenewa amalola kaamba ka aja onse obadwa mkati mwa nthaŵi ya zochitika za m’mbiri yakale ndi aja onse omwe anali ndi moyo pa nthaŵi imeneyo.

J. A. Bengel walongosola mu New Testament Word Studies yake kuti: “Ahebri . . . amaloza ku zaka makumi asanu ndi ziŵiri mphambu zisanu kukhala monga mbadwo umodzi, ndipo mawu akuti siudzapita, amagwirizanitsa kuti mbali yokulira ya mbadwo umenewo [wa tsiku la Yesu] ndithudi, koma osati wonsewo, ukakhala utapita zonsezo zisanakwaniritsidwe.” Ichi chinakhala chowona pofika chaka cha 70 C.E. pamene Yerusalemu anawonongedwa.

Mofananamo lerolino, ambiri a mbadwo wa 1914 anamwalira. Komabe, pakali mamiliyoni angapo pa dziko lapansi omwe anabadwa m’chaka chimenecho kapena chisadakhale. Ndipo ngakhale kuti chiŵerengero chawo chikuzimiririka, mawu a Yesu adzakhala owona, “mbadwo uwu ndithudi sudzatha kufikira zinthu zonsezi zitachitika.” Ichi chirinso chifukwa china cha kukhulupirira kuti tsiku la Yehova longa mbala liri pafupi. Chotero, ndi zochitika zotani zimene Akristu ogalamuka ayenera kuyang’anira?

“Mtendere ndi Chisungiko” Posachedwapa?

“Pakuti inu nokha mudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Nthaŵi iriyonse pamene adzanena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ kenaka chiwonongeko cha mwadzidzidzi chidzawagwera mwamsanga.”—1 Atesalonika 5:2, 3, NW.

Chiyambire mapeto a Nkhondo ya Dziko II mu 1945, mtundu wa anthu wadzandira pandunji penipeni pa nkhondo pamene mphamvu ziŵiri zotsutsana, United States ndi Soviet Union, zakangana wina ndi mnzake. Vuto la mamisailo a ku Cuba la mu 1962 linali ngozi ya kulalirana kwachindunji. Koma Soviet Union inachotsa mamisailo ake kuchoka ku Cuba, ndipo United States mwakachetechete inachotsa mamisailo ake ku Turkey. Uku kunali kokha kumodzi kwa kuwonetsera kochulukira kwa Nkhondo Yoputana ndi Mawu.

Kuleka kugwiritsira ntchito zida za nkhondo kwakhala nkhani kaamba ka kukambitsirana kwa zaka makumi angapo ndipo nthaŵi zambiri kwangotha mkachitidwe ka nthanthi kaamba ka maiko onsewo. Tsopano, m’miyezi yothera ya nyengo ya Prezidenti Reagan ndi malamulo a mkhalidwe wakugwa kwa Mlembi Gorbachev otchedwa glasnost (kufikirika), pakuwonekera kukhala kukambitsirana kolimba konena za kuthetsa mkhalidwe wa zida za nyukliya. Kaya ichi chiri chiyambi cha kubweretsa mtendere ndi chisungiko cholinganizidwa kaamba ka dziko lonse, sitingathe kuwoneratu. Koma mogwirizana ndi ulosi wa Baibulo, chimenecho ndi chimene Akristu akuyembekezera. Pamene chachitika, kenaka chiyani?

Ophunzira osamalitsa a Baibulo sadzanamizidwa “nthaŵi iriyonse pamene iwo adzanena kuti: ‘Mtendere ndi chisungiko!’”—kaya chidzachokera ku Mitundu Yogwirizana kapena mphamvu zazikulu izo zeni zodziimira pa zokha. Baibulo limasonyeza mowonekera bwino kuti mtendere weniweni ndi chisungiko zingadze kokha kuchokera ku ulamuliro wa chilungamo, boma la Ufumu wa Mulungu mwa Kristu.

Kaamba ka chifukwa chimenecho kulengeza kwapadera kwa kutsogolo kwa dziko lonse kwa mtendere ndi chisungiko kochitidwa ndi atsogoleri a dziko kudzakhala chizindikiro kaamba ka Mulungu kuyamba kugwira ntchito, “ndendende monga mbala usiku,” akumafikira dziko losakhulupirira mwadzidzidzi. Inde, “chiwonongeko chadzidzidzi” kenaka chidzagwera mphamvu za chipembedzo ndi za ndale zadziko zomwe zaipitsa Yehova ndi mboni zake. Kodi timadziŵa chimenecho motani?

Kachitidwe Kosankha ka Wokwera pa Kavalo Woyera

Kubwerera ku masomphenya a amuna anayi okwera pa kavalo a Chivumbulutso, pali wokwera mmodzi yemwe sitinatchule—woyambirira, wokwera pa kavalo woyera. Baibulo limamlongosola iye: “Ndipo ndinapenya, ndipo tawonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nawo uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” Uyu ali mmodzimodzi yemwe walongosoledwa mu mutu 19 wa Chivumbulutso: “Ndipo tawonani kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo aŵeruza, nachita nkhondo molungama. . . . Ndipo mkamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo.” Ndipo kodi ndani ameneyu? Cholembedwa chimodzimodzicho chimatiwuza kuti iye ali ndi dzina lolembedwa, “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” Iye ali Mwana wowukitsidwa wa Mulungu, Kristu Yesu.—Chivumbulutso 6:2; 19:11-16.

Kenaka, nchiyani, chomwe chimaitanira kaamba ka ntchito ndi “Mfumu ya mafumu imeneyi?” Nsonga ikufikiridwa pamene “mfumu ya kumpoto” (gawo losakhala la chicapitalist) ndi “mfumu ya kum’mwera” (mitundu ya chicapitalist yolamulidwa ndi United States), yowunikiridwa mu Danieli mutu 11, ifika pa chimake. (Monga mmene Danieli 11:40 ananeneratu “mfumu ya kumpoto” yafalikira kale m’maiko ambiri, makamaka chiyambire 1945.)a

Chotero, kodi nchiyani chinanso chimene chifunikira kuchitika kuloŵereramo kogamulapo kwa Mulungu kusanachitike kwa kubweretsa mapeto ku dongosolo la kachitidwe ka zinthu liripoli?

Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti panthaŵi ina mbali ya ndale zadziko mu Mitundu Yogwirizana idzawukira chipembedzo cha dziko chochita malonda ndi kuchivula icho, kuwononga mphamvu zake ndi kulamulira kwake pa anthu okhulupirira malaulo.—Chivumbulutso 17:16, 17.b

Kuwononga kumeneku kwa mbali za chipembedzo chonyenga cha dziko mosakaikira kudzakhala monga chiyambukiro kuwukira pa Mboni za Yehova. Chimenechi kenaka chidzayambitsa kuwukira kochitidwa ndi Mfumu ya Yehova, Wokwera wa pa kavalo woyera. (Ezekieli 38:10-12, 21-23) Ndipo kodi nchiyani chimene Danieli 2:44 imanena ponena za chotulukapo chake? “Ndipo masiku a mafumu aja [mphamvu za ndale zadziko zamakono] Mulungu Wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.” Inde, nkhondo ya Mulungu ya Harmagedo motsutsana ndi mbali zowoneka ndi maso za ndale zadziko za Satana pa dziko lapansi idzatulukapo m’chipambano chotheratu kwa Yehova ndi Mfumu yake ya mafumu.—Chivumbulutso 16:14-16; 19:17-21.

Kodi nchiyani chomwe chidzatsatira? Nkulekeranji, chikhumbo chokhalitsa cha Akristu okonda mtendere, owopa Mulungu—Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa boma la Ufumu wa Mulungu pa mtundu wa anthu omvera! Kenaka adzakwaniritsidwa malonjezo aulemerero a Chivumbulutso 21:3, 4: “Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”

Ngati inu mungafune chidziŵitso chowonjezereka ponena za maulosi a Baibulo ozizwitsa amenewo ndi chimene amatanthauza kaamba ka ife mwaumwini, chonde fikirani Mboni za Yehova m’dera lanu kapena lemberani kwa ofalitsa a magazini ino m’dziko lanu.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka kulingalira kwa tsatanetsatane kwa kuwombana kumeneku, onani bukhu lakuti “Your Will Be Done On Earth,” mutu 11, “The Appointed Time of the End,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Kaamba ka kulingalira kwa tsatanetsatane kwa ulosi umenewu, onani chofalitsidwa cha Watchtower “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules!, mutu 26, “The Judgment Upon the Great Harlot,” lofalitsidwanso ndi Watchtower Society.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Mbadwo—“Unyinji wonse pamodzi wa awo obadwa pa nthaŵi imodzi, mofutukulidwa kuphatikizapo aja onse okhala pa nthaŵi yopatsidwa.”—“A Greek-English Lexicon of the New Testament”

[Mawu Otsindika patsamba 16]

Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti mbali za ndale zadziko mu Mitundu Yogwirizana zidzatembenuka molimbana ndi chipembedzo chochita malonda

[Chithunzi patsamba 15]

Pambuyo pa Harmagedo, mu dziko la Mulungu latsopano la mtendere ndi chilungamo, ‘zoyambazo zidzakhala zitapita.’—Chivumbulutso 21:3, 4

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena