Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 6/8 tsamba 17-18
  • Chikhumbo Kaamba ka Ndalama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhumbo Kaamba ka Ndalama
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pa Ulendo—Kaamba ka Ndalama
  • Maiko Otukuka Kumene
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kugula Chimwemwe Popanda Ndalama
    Galamukani!—1988
  • Ndalama
    Galamukani!—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 6/8 tsamba 17-18

Chikhumbo Kaamba ka Ndalama

Ndi mlembi wa Galamukani! mu Britain

‘CHONULIRAPO CHANGA,’ anavomereza tero Julian kuchokera ku Philippines, ‘chinali kukhala mponda matiki podzafika nthaŵi imene ndinali wa zaka 45.’ Karel, kuchokera ku South Africa, wavomereza kuti, “ndinadzazidwa ndi chifuno cha kukhala wolemera.”

Ndithudi, si onse, m’chenicheni, omwe amafuna kukhala a mponda matiki koma amakhumba kukhala ndi chuma chokwanira ndi ndalama kusangalala ndi moyo ndi kuchita chimene iwo amafuna. Uwu unali mkhalidwe wa munthu wa malonda wa ku Japan Kichisaburo yemwe ananena kuti, “Ndinaganiza kuti zinthu zimenezi zikatsogolera ku chimwemwe.”

Liz, kuchokera ku Canada, anadzimva mofananamo. “Monga munthu wachichepere,” iye akusimba kuti, “Ndinakhulupirira kuti ndalama zimabweretsa ufulu kuchokera ku chisoni.” Mwamuna wake, Tom, anayembekeza kuti ndalama zikakhoza kumthandiza iye “kupulumuka m’zonsezo, . . . kumene kungakhale kulibe upandu, kulibe kuipitsidwa kwa mpweya, kulibe anthu a mitima iŵiri ochita nawo.”

Pa Ulendo—Kaamba ka Ndalama

Kupyola m’mbiri yonse, anthu ofunafuna chuma akhala ali pa ulendo. Masiku amaulamuliro akumbuyo, amuna amalonda a ku Britain anatsatira mosataya mtima kumbuyo kwa anthu oyendera maiko kukafunafuna chuma cha m’nthaka cha makontinenti onse, onga ngati Africa. Kenaka, ndi kugwa kwa ulamuliro ndi mavuto a za chuma a posachedwapa, kayendedweko kakhala kakubwerera m’mbuyo kaŵirikaŵiri popeza kuti nzika za Commonwealth zimapita ku Britain, osati moyenerera kuti zikalemere, koma kukapanga ndalama zokwanira za kuchirikiza mabanja awo.

Amuna zikwi zingapo ndi akazi amachoka ku Philippines m’kufunafuna ntchito m’malo ena, ndipo ambiri amapeza ntchito m’mizinda ya Persian Gulf ndi kwina kulikonse. Anthu a ku Mexico ndi ambiri ochokera ku Central ndi South America amapita cha kumpoto ndi chiyembekezo cha kufuna kupeza ndalama mu United States. Maiko ambiri a ku Europe amakhala olandira anthu ochokera ku Middle East ndi North Africa.

Mogwirizana ndi Manpower Review ya ku South Africa ya January 1987, chiŵerengero cha olowa m’dziko olembetsedwa mwalamulo kumeneko chinali 371,008 pa June 30, 1985. Ngakhale kuli tero, ripotilo likuwonjezera kuti, “pali kuyerekeza kwa 1.5 miliyoni opanda lamulo omwe alowa mu South Africa kukatha china cha chuma chake.”

Ngakhale mkati mwa mitundu yamakono yolemera kwambiri, anthu akuyenda kukapanga ndalama. Ichi chiri chowona mu Britain. Anthu ochulukirapo akugwira ntchito kum’mwera ndi kusunga nyumba zawo kumpoto. Kuchitira chitsanzo chifukwa chake, nyumba yokhalamo chapakati pa London (chakum’mwera), yolongosoledwa kukhala “msasa [nyumba],” yokhala kokha ndi malo a mapazi 61 mbali zonse zinayi, posachedwapa inabwera pa msika pa mtengo wa unyinji wa $54,000, [U.S.] Komabe, unyinji wa ndalama umenewo umagula nyumba ya zipinda zogonamo zitatu mkati mwa makilomita 130 mu London.

Pali nzika za ku Asia 60,000 zokhala ku Bradford, mzinda wa kumpoto kwa England. Ochulukira a olowa m’dziko amenewa anabwera ku malo apakati a indastri amenewa kukagwira ntchito m’makina ake okonza thonje. Koma pamene makina odzigwirira ntchito paokha achepetsako anthu ogwira ntchito, osalembedwa ntchito tsopano amadalira pa kulipilira kwa chisungiko cha mayanjano a boma kaamba ka khalidwe lawo. Chotero, ambiri amapeza kuti chikhumbo chawo kaamba ka ndalama chimathera m’chisoni.

Maiko Otukuka Kumene

Mofananamo, m’maiko otukuka kumene, chiyembekezo cha ntchito yokhazikika chimakoka zikwi zingapo kuchoka m’nyumba zawo m’mbali za ku midzi kupita ku mizinda. Zowona, ambiri amapeza ntchito. Koma kodi malipiro awo amabweretsa chimwemwe?

Malipiro ochepa omwe ogwira ntchito amalandira amafunikira choyamba kulipira renti yomakwera kaŵirikaŵiri ya nyumba zomangidwa mumkhalidwe wa m’mizinda, mothekera m’malo auve omwe amazungulira mizindayo. Zotsalapo zimafunikira kufikiritsa zifuno zodidikiza za anansi awo omwe ali kumudzi. Mu Africa, mwachitsanzo, pamapeto pa mwezi, mapositi ofesi ambiri a m’mizinda amakhala odzala ndi mizere ya anthu ondandama kuti agule money order kaamba ka anansi awo owadalira omwe ali kumidzi.

Ngakhale pamene mabanja akhala pamodzi m’mizinda, zipsyinjo zowonjezereka zina za ndalama zimadidikiza. Ndalama zimafunikira kuikidwa pambali kaamba ka kusamalira umoyo, kaamba ka kuyendera, kaamba ka ndalama za ku sukulu, kaamba ka chakudya, ndi kaamba ka misonkho ya nyumba. Ndandandayo imawonekera kukhala yopanda polekezera. Chiri chosadabwitsa kuti okhala m’mizinda ambiri amakhala ndi ntchito ziŵiri.

Kodi ichi chimawonekera kukhala chothandizira kaamba ka chimwemwe? Kutalitali. Chotero, kenaka, kaya musamuka kapena kukhala kumene muli, funso limakhalabe, Kodi ndi malo otani amene ndalama imachita m’moyo wanu? Yankho liri lofunikira koposa ku chimwemwe chanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena