Kuphunzira Kuchokera kwa Mboni
Chimenecho ndi chimene ndemanga ya mkonzi mu nyuzipepala ya Norway Troms Folkeblad ya pa July 15, 1986, inanena kuti ambiri akayenera kuchita. “Misonkhano ndi makonzedwe omwe ali nawo ali chifupifupi angwiro mumkhalidwe wawo ndi kulongosoka. Palibe chirichonse chochitidwa mwa mwaŵi,” nkhaniyo inadziŵitsa tero.
“Chipambano cha magulu a za maseŵera ndi zopangapanga za magulu a achichepere kaŵirikaŵiri chimadalira pa kufunitsitsa kuthandiza kwa chiwalo chirichonse. Awa ayenera kuwona njira imene Mboni za Yehova zimalinganizira zochitachita zawo. Zambiri zingaphunziridwe mwa kuyang’ana mzimu wofunitsitsa womwe izo zimasonyeza. Chiri chifupifupi chosakhulupirika.”