Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 32
  • “Yankho ku Mavuto Athu Onse”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yankho ku Mavuto Athu Onse”
  • Galamukani!—1988
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 32

“Yankho ku Mavuto Athu Onse”

Zimenezo ndi zimene munthu wachichepere wa ku Puerto Rico akunena kuti zimapezeka m’bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It. Iye akulemba kuti:

“Si kale kwambiri pamene ndinakulemberani ponena za vuto lomwe ndinali nalo, kuchita mpsyotompsyoto, ndipo ndinakufunsani kuti mundikomere mtima ine ndi chithandizo china mwa kugwiritsira ntchito kufalitsa chidziŵitso china m’magazini yanu. Chabwino, bwenzi langa, mmodzi wa Mboni za Yehova, anandipatsa ine bukhu lakuti Your Youth—Getting the Best out of It kuti ndiŵerenge. Ichi chinachitika chifupifupi mwezi umodzi wapitawo. Ndikufuna kukulolani inu kudziŵa kuti chiyambire pamene ndinaŵerenga mutu 5 wa bukhuli, sindinachitepo chizoloŵezichi kachiŵirinso. Ndazindikira kuti kuchita mpsyotompsyoto ndithudi sikuli chinachake chimene wina amafunikira. . . .

“Ndingakonde ngati munthu wachichepere aliyense angaŵerenge bukhu limeneli mosasamala kanthu za unansi wake ndi chipembedzo. Anthu achichepere onse ali ndi mavuto ofananawo, ndipo bukhu limeneli liri ngati chuma, popeza kuti liri ndi yankho ku mavuto athu onse. . . . Mufunikira kupitirizabe kufalitsa mabukhu kaamba ka achichepere chifukwa chakuti m’dziko lodzaza ndi anamgoneka ndi chisembwere, bukhu limeneli liri ngati galasi yodzaza ndi madzi ozizira kwambiri, otsitsimula.”

Pa mbali pa kukambitsirana kwa kuchita mpsyotompsyoto ndi kugonana kwa ofanana ziwalo, bukhu limeneli limakwaniritsa kugwiritsira ntchito kwa anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa, maseŵera, nyimbo, kuvina, kupita kocheza, kutomerana, ndi nkhani zina zambiri zomwe zimayambukira achichepere. Landirani kope mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi chopereka cha K8.00.

Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Your Youth—Getting the Best out of It. Ndatsekeramo K8.00 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena