Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 9/8 tsamba 30-31
  • Kodi Iwo Akuyambukitsa Imfa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Iwo Akuyambukitsa Imfa?
  • Galamukani!—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kusuta Kulidi Koipa Motero?
    Galamukani!—1991
  • Ndudu za Fodya Kodi Mumazikana?
    Galamukani!—1996
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Ogulitsa Imfa—Kodi Ndinu Wogula?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 9/8 tsamba 30-31

Kodi Iwo Akuyambukitsa Imfa?

“CHENJEZO: Dokotala Wotumbula Wamkulu Wagamulapo Kuti Kusuta Fodya Kuli Kowopsya ku Umoyo Wanu.” Wosuta fodya nthaŵi zonse mu United States amakana chenjezo lofunikali losindikizidwa pa mapaketi a ndudu. Kwa oterewa, kansa ya mapapo imawoneka, moipirako, chiwopsyezo chapatali. ‘Zingakhale zitani,’ oterowo amalingalira tero, ‘liri thupi langa.’

Komabe, American Cancer Society yachitira ripoti kuti: “Osuta fodya amaika m’ngozi osati kokha umoyo wawo komanso umoyo wa awo owazungulira.” Chofalitsidwa cha chiDutch Roken welbeschouwd (Kusuta—Zinthu Zonse Zalingaliridwa) chimagwirizanitsa, kulingalira kuti munthu wosasuta yemwe akugwira ntchito limodzi ndi wosuta fodya wa nthaŵi zonse angakhoze kulowetsa mlingo wofananawo wa zidutswa zovulaza mofanana ndi munthu wosuta ndudu zisanu pa tsiku! Sichiri chodabwitsa, kenaka, kuti osasuta omwe agwira ntchito m’malo a anthu osuta kwa zaka zoposa 20 kaŵirikaŵiri amavutika ndi chifuŵa—monga ngati kuti anali kusuta ndudu imodzi kufika ku khumi pa tsiku!

Chifukwa chake? Utsi wa pambali. Mmenemo ndi mmene ofufuza amaitanira utsi wotuluka kuchoka kotsirizira kwa ndudu yoyatsidwa. Kutalitali ndi kukhala wosavulaza, utsi wa pambali uli ndi ululu wochulukira ndi nicotine kuposa utsi womwe umasutidwa! Ofufuza amadzinenera, ngakhale ndi tero, kuti osuta mu United States angakhale ndi thayo bwino lomwe kaamba ka imfa zirizonse kuchokera pa 5,000 kufika ku 50,000 za osasuta chaka chirichonse.

Dundu, Akazi, ndi Makanda. Palinso kudera nkhaŵa komakulakulabe kwakuti kusuta fodya kumayambukira makanda mokulira. “Kusuta kwa anthu okhala ndi pakati,” kachenjeza tero kabukhu kakuti Facts and Figures on Smoking, “kuli ndi ziyambukiro zachindunji, ndi zobweza mbuyo ku kakulidwe ka kamwana kosabadwa ndipo kungayambukire moipa kakulidwe ka mwanayo, kakulidwe ka luntha, ndi makhalidwe.” Akazi apakati omwe amasuta amalowetsa unyinji wokulira wa utsi wovulaza m’mwazi woyenda m’mitsempha ya ana awo osabadwa. Zoyerekezera zimasiyanasiyana, koma ena amayerekeza kuti pa kubadwa, makanda awo amalemera, pa avereji, magramu mazana aŵiri kuchepera pa makanda a anthu osasuta.

Phunziro lotsogozedwa mu Denmark linalingalira mowonjezereka kuti kusuta fodya kungakhozenso kubweza mbuyo kuyesayesa kwa akazi kwa kuyamwitsa ana. “Mwinamwake monga chotulukapo cha nicotine,” atero ofufuza a chiDanish, “osuta mopambanitsa ali ndi mlingo wochepera wa mphamvu za mkati, tsatanetsatane yemwe amabweretsa kutulutsidwa kwa mkaka.”

Moyerekezera, ngakhale ndi tero, akazi ochulukira akusuta fodya lerolino—ndipo kusuta ndudu zochulukira—kuposa ndi kalelonse. Monga chotulukapo chake, yatero Facts and Figures on Smoking, kansa ya mapapo mu United States yapambana kansa ya maŵere monga kansa ya kupha yopambana ya akazi. Iyo inatenga miyoyo yoyerekezedwa pa akazi 40,000 mu 1985 mokha.

Kusintha kwa Mkhalidwe. Ngakhale kuli tero, pali siliva lokhala pa mtambo wa utsi umenewu. Mogwirizana ndi American Cancer Society, ndemanga molimbana ndi kusuta zikukula. Anthu atatu mwa anayi a ku America tsopano amadzimva kuti osuta fodya sayenera kusuta pakati pa ena. Chiŵerengero cha anthu omwe sakusutanso chikukula mofananamo. Kusuta kwa ndudu zonse mu United States ndi Kumadzulo kwa Europe kukutsikirako. Watero Adele Paroni, wolankhulira wamkazi wa American Cancer Society: ‘Mbiri yabwino koposa iri yakuti tsopano ochepera pa achikulire 30 peresenti a ku America amasuta!’

Padakali anthu ena 54 miliyoni mu United States omwe amasuta fodya. Koma mogwirizana ndi American Lung Association, osuta fodya asanu ndi anayi mwa khumi akunena kuti akufuna kuleka. Mwinamwake adzasonkhezeredwa ndi machenjezo atsopano, enieni osindikizidwa pa mapaketi a ndudu. Ena a iwo amaŵerenga kuti: “CHENJEZO LA DOKOTALA WOTUMBULA WAMKULU: Kuleka Kusuta Fodya Tsopano Kumachepetsa Mokulira Ngozi Yowopsya ku Umoyo Wanu.”

[Zithunzi patsamba 31]

Utsi wa pambali kuchokera ku ndudu uli ndi ululu wochulukira ndi nicotine kuposa utsi womwe umasutidwa

Akazi apakati omwe amasuta amaloŵetsa unyinji wokulira wa utsi wakupha m’mwazi woyenda m’mitsempha ya ana awo osabadwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena