Mmene Ukwati Uwu Unapulumutsidwira
“Kugwiritsiridwa ntchito kwa uphungu wa m’bukhu lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe kunapulumutsa ukwati wanga,” analemba tero muŵerengi woyamikira wa ku South Africa. “Mutu 5, ‘Mkazi Amene Ali Wokondedwa Kwambiri,’ unatsegula maso anga. Sindinaganizire konse m’maloto anga oipa kuti ndingachititse mavuto ambiri chotero popanda kulingalira. Ndikuyamikirani kwabasi. Ukwati wanga unali m’mbali za mafunde kwenikweni a m’nyanja, ndipo tsopano, pambuyo pa miyezi ingapo, wabwereranso pa doko la bata lachimwemwe.”
Ngati inu mukukhumba thandizo m’kupangitsa ukwati wanu kukhala wachimwemwe koposapo, mungapindule kuchokera m’bukhu limeneli. Landirani kope mwa kudzaza ndi kutumiza kapepalaka.