Ngozi za Umoyo Ngakhale M’malo a “Osasuta”
THE Journal of the American Medical Association (JAMA), February 10, 1989, inasimba kuti: “National Academy of Sciences inabwereramo mu tsatanetsatane wa kusuta utsi wapambali . . . , ikumalankhula mwachindunji ku malo ozungulira a kuwuluka kochitidwa ndi makampani a ndege.” Chiyamikiro chinali cha: “Kuletsa kusuta mu ndege zonse za kumaloko za malonda kaamba ka zifukwa zazikulu zinayi: kuchepetsako mkwiyo, kuchepetsako ngozi ku umoyo, kuchepetsako ngozi za moto, ndi kubweresta ubwino wa chiwiya chotulutsa ndi kuloŵetsa mpweya m’chigwirizano ndi miyezo ya malo otsekeredwa ena.”
Phunziro lakuya la academy imeneyo linavumbula kuti: “Kuwunikiridwa ku chikonga kopimidwa mkati mwa kuwuluka ndi ndege kogwiritsira ntchito ziwiya zofufuzira kuwunikiridwa kwaumwini kunapezeka kukhala kosiyanasiyana, kokhala ndi malo ena okhalako osasuta akupezeka ndi mlingo wolingana ndi uja wa m’malo a osuta. Akalinde ogawiridwa kugwira ntchito m’malo a osasuta anali osachinjirizidwa ku kuwunikiridwa ku utsi.”
Phunzirolo linasonyeza kuti “mlingo wa mpweya wa chikonga unali wosiyanasiyana mwakuya, wokhala ndi malo ena a osasuta akumakhala ndi mlingo wokulira kuposa uja wa m’malo a osuta” ndipo inakumbutsa aŵerengi kuti “ziyambukiro zoipa za umoyo pa osasuta a mpweya wapambali, kapena osafuna, kusuta kumaphatikizapo kansa ya mapapo ndi matenda a ziŵalo zopumira.”
Kope imodzimodziyi ya JAMA inasimba phunziro lomwe linakhazikitsa mphamvu yomwereketsa ya chikonga, ikumanena kuti: “Anthu ofunafuna kuchiritsidwa kwa kudalira pa anam’goneka anakhoterera pa kukhala ndi chilakolako cha ndudu ndi kukhala ndi vuto la kuleka ndudu likumakhala lokulira kapena lopambana tsatanetsatane wokulira wa vuto lawo [zakumwa zoledzeretsa, cocaine, heroin].”
Canada inaletsa kusuta m’kuwuluka ndi ndege kwa maora aŵiri kapena ocheperapo mu 1987. Makampani onse aŵiri andege a ku Canada anapita kuposa apo, akumaletsa kusuta mkati mwa kuwuluka m’ndege zawo zonse za ku North America. Mu United States, bungwe la lamulo laletsa kusuta pa kuwuluka kofupikira, ndipo “kampani imodzi ya ndege ya ku US yaletsa mwaufulu kusuta pa kuwuluka ndi ndege kwa utali uliwonse mkati mwa United States, kusiyapo kuwuluka ndi ndege kopita ndi kuchokera ku Hawaii.” Pamene makampani andege owonjezereka atenga malamulo ofananawo a kusasuta adzathandizira kuchepetsako ngozi za kuwuluka.