1914—Posinthira
Olemba mbiri amanena kuti 1914 inali posinthira m’mbiri. Komabe Baibulo kalekale kwambiri linali litaneneratu kuti ikakhaladi. Kodi nchiyani chimene Baibulo limanena ponena za 1914? Kodi ndimotani mmene inu mwayambukiridwira ndi zimene zinachitika panthaŵiyo?
Mayankho osangalatsa aperekedwa m’bukhu lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? Onani mutu wakuti “Chaka Chosonyezedwa—1914 C.E.,” woyamba pa tsamba 70. Bukhu limeneli, lomwe linakonzedwanso mu 1986, kufika pa nthaŵi ino lafikira kugawiridwa kozizwitsa kwa makope oposa 39 miliyoni m’zinenero 69. Pezani kope lanu. K10 yokha.
Chonde Tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 192 lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? Ndatsekeramo K10 (Zambia).
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
U.S. National Archives photo