Tsamba Lachiŵiri
M’njira zambiri dziko lataya makhalidwe owona. Koma bwanji poneza za inu? Kodi mumachitira monga zinyalala makhalidwe amene atsimikizira kukhala aphindu mkati mwa zaka mazana angapo? Kapena kodi mwanzeru mumasunga chitini chanu cha zinyalala kaamba ka zinyatsi ndi kusunga makhalidwe kukhala mphamvu yotsogoza m’moyo wanu?