Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 8/8 tsamba 20-21
  • “Sitipatsa Mlandu Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sitipatsa Mlandu Mulungu”
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubale wa Dziko Lonse
  • Kodi Anthu Amafunadi Mulungu Kusalola Kuipa?
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
  • “Yembekezera Yehova”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • “Yehova Sadzasiya Anthu Ake”
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 8/8 tsamba 20-21

“Sitipatsa Mlandu Mulungu”

PAMENE ndege ya Pan American 103 inaphulitsidwa mumlengalenga ndi zigawenga December yatha yokhala ndi anthu 259 okweramo, bishopu wa Roma Katolika wa ku Galloway, Maurice Taylor, anali ndi mawu oipa kaamba ka Mulungu:

“Atate, ngati Inu muli Mulungu wachikondi, nchifukwa ninji Inu munalola ichi kuchitika? Nchifukwa ninji Inu munalola chiwonongeko cha miyoyo yopanda liwongo mazana angapo? Nzika 10 zomwe zinali za Lockerbie? Unyinji wochulukira omwe anali asanamvepo za Lockerbie, koma amene miyoyo yawo inatha moipitsitsa chotero m’makwalala ndi m’minda ya mbali imeneyi ya Scotland? Ndipo nchifukwa ninji Inu mumalola anthu ochulukira chotero kuvutika ndi katundu wa tsoka woipa chotero mwa kutaikiridwa?”

Unyinji wa ophunzira ochokera ku Yunivesiti ya Syracuse mu United States anali pakati pa minkholeyo. Mildred Sachuck, mayi wa panyumba pa imodzi ya sukulu zake, ananena za zigawenga zomwe zinatchera bombalo kuti: “Tifunikira kuwapheratu iwo.”

Ripoti la nkhani limodzi linanena kuti: “Kalinde wa m’ndegeyo Paul Garrett, wa zaka 41, anakonzekera kutsegula malo ogulitsira zinthu mu Paris pambuyo pa zaka 15 za kukhala ndi kampani ya ndegeyo. ‘Tsoka loipitsitsa liri lakuti uku kunafunikira kukhala kuwuluka kwake m’ndege kotsirizira,’ anatero Jan MacMichael, bwenzi lokhala mu Millbrae, Calif[ornia].”

Kachitidwe ka makolo a Paul, Ernest ndi Nadine Garrett, Mboni za Yehova zokhala mu Millbrae, kanali kosiyana kwenikweni ndi kachitidwe ka bishopu wa ku Galloway ndi mayi wa panyumba wa ku Syracuse. Kachitidwe ka makolo a Paul kanawunikiridwa m’kalata yomwe iwo anatumiza m’kuyankha ku zitonthozo zolandiridwa kuchokera ku Mboni inzawo mu Mzinda wa New York:

Ubale wa Dziko Lonse

“Ndi chokondeka chotani nanga kwa inu, Karl, kupeza nthaŵi kuchokera ku ndandanda yanu yotanganitsidwa kutitumizira ife kalata yotonthoza chotero. Iri imodzi ya ambiri. Tamva kuchokera kwa Mboni mu Norway, Italy, France, England, ndi Cameroon—chifupifupi makardi 600, matelegramu, ndi makalata, ndi kutumiziridwa lamya koposa pa 250 kuchokera kuzungulira dziko. Paul anadziŵa anthu ochulukira kwenikweni, pokhala kalinde wa mu ndege kwa zaka zambiri chotero ndi kampani ya ndege ya Pan American. Mautumiki achikumbikiro anachitidwira mu Paris, San Francisco, ndi mu Jacksonville, Florida, okhala ndi chiwonkhetso chonse cha opezekapo 1,385.

“Mboni za kumaloko za mu mpingo wathu ndi mipingo yapafupi zinasamalira nyumba yathu ndi kugula zakudya, kuphika ndi kukonzekera icho, kuyeretsa nyumba yathu, kusinthanasinthana m’kugona m’nyumba yathu, osatisiya tokha ife nkomwe kwa nthaŵi ya nyengo ya milungu iŵiri kuti atsimikizire kuti tinali bwino. Mowonadi, Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse ziri ndi ‘chikondi pakati pawo.’—Yohane 13:35.

“Woimira Pan American yemwe anagawiridwa ku banja lathu kupereka chitonthozo ndi kulimbikitsa anachitira ndemanga kuti: ‘Ndadza kudzakutonthozani anthu inu, koma ndatonthozedwanso m’malomwake. Pali chinachake chosiyanako ponena za anthu awa kuchokera kwa anthu ena omwe ndawona pa zochitikazi.’ Pamene mkaziyo anafunsidwa chimene anatanthauza, iye ananena kuti: ‘Anthu awa mowonadi amasamalira kaamba ka wina ndi mnzake.’

“Tiri oyamikira kuti timamvetsetsa Baibulo ndi kudziŵa kuti ‘nthaŵi ndi zochitika zosayembekezereka’ zimawagwera. (Mlaliki 9:11, NW) Kumvetsetsa chimenechi, Karl, sitingakhoze mosalungama kutonza Mulungu kapena kumunyoza iye kaamba ka tsoka limeneli, monga momwe bishopu Wachikatolika wa ku Galloway anachitira. Ayi, sitipatsa mlandu Mulungu kaamba ka imfa ya mwana wathu. Bishopuyo, m’chenicheni, akunena kuti Yehova sali Mulungu wachikondi.—1 Yohane 4:8.

“Ndipo sitimafunanso kubwezera choipa molimbana ndi zigawengazo, monga momwe anachitira mayi wa panyumba pa sukulu ya pa Syracuse yomwe inatayikiridwa chiŵalo m’kugwako, yemwe ananena kuti: ‘Tifunikira kuwapheratu iwo.’ Nkhani zoterozo timazisiyira kwa Mulungu, yemwe akunena kuti: ‘Kubwezera kuli kwanga; ine ndidzabwezera.’—Aroma 12:19.

“Ndipo chotsirizira, koma osati chokhacho, chiri chiyembekezo chabwino koposa cha kuwukitsidwa chomwe chidzatilimbitsa ife tsiku lirilonse kufikira titawona mwana wathu wokondedwa kachiŵirinso. ‘Ngati munthu amwalira, kodi iye angakhalenso ndi moyo?’ anafunsa tero mwamuna Yobu kalelo. Chabwino, Baibulo linayankha funso limenelo pa Yesaya 26:19: ‘Akufa anu adzakhala ndi moyo . . . Adzawuka.’ Timapeza chitonthozo kuti mwana wathu anamwalira wokhulupirika monga mmodzi wa Mboni za Yehova, wokhala ndi dzina labwino ndi Mulungu, dzina lomwe Iye adzakumbukira pa nthaŵi ya chiwukiriro. (Mlaliki 7:1, [NW] mawu am’munsi; Yohane 5:28) Ife motsimikizirika timadzimva achisoni pa kutayikiridwa kwa mwana wathu, koma pokhala ndi chiyembekezo cha chiwukiriro, ‘sitimalira monga otsalawo.’”—1 Atesalonika 4:13.

Paul wasiya mkazi wake, Dominique. Iye amakhala mu Paris, France, ali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo amadzimva monga mmene amachitira makolo a Paul. Iye nayenso samapatsa mlandu Mulungu kaamba ka tsoka lake la kutayikiridwa ndipo amayang’anizana ndi mtsogolo ndi kulimba mtima ndi chiyembekezo.

Kodi Anthu Amafunadi Mulungu Kusalola Kuipa?

M’nthaŵi zakale mwamuna wotchedwa Yobu ankapyola m’masoka osati ochitidwa ndi Yehova, komabe iye anatonza Yehova ndi funso iri: “Kodi chiri chabwino kaamba ka inu kuchita cholakwika?’’ Yehova anamyankha iye ndi funso lina: “Udzatsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?” (Yobu 10:3, NW; 40:8) Kuti alangize Yobu, Mulungu anabwereramo m’zochulukira za chilengedwe Chake m’mwamba ndi padziko lapansi zomwe zinawunikira mikhalidwe Yake ya chilungamo, nzeru, mphamvu, ndi chikondi. (Yobu, mitu 38-41) Yobu anazindikira chimo lake ndi kudera nkhaŵa kwake, akumanena kuti: “Chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.”—Yobu 42:6.

Mwa kuchimwa kwawo, anthu amadzibweretsera masoka ochulukira pa iwo eni ndi ena. Iwo amalalikira motsutsana ndi kulola kwa Mulungu kuipa pamene iwo ponse paŵiri amalola iko ndi kukuchita. (Yerekezani ndi Aroma 2:1, 21-24.) Kuipa kwawo kumatenga mitundu yambiri—kunama, kunyenga, kuba, kutsendereza, kuchita dama, kuchita chigololo, kugonana kwa ofanana ziŵalo, kupha, kupanga mfuti ndi mabomba, kuyambitsa nkhondo ndi zisinthiko, zonsezo zitawazidwa mwaufulu ndi kudzilungamitsa, zinyengo, ndi mwano. Asayansi ena a zamayanjano afikira pa kutsutsa kuti zitaganya, mwa kunyada kwawo ndi kutsendereza kwa magulu ena, zayambitsa nthaka mu imene kuwukira kumabuka, ndipo osoŵa chochita mosakhululukidwa angakhale zigawenga zopenga, akumapha opanda liwongo osaloŵetsedwamo. (Yerekezani ndi Eksodo 1:13, 14; 1 Mafumu 12:12-14, 16, 19; Mika 7:3, 4; Mateyu 7:12.) Motsimikizirika Mlaliki 8:9 imalankhula chowonadi pamene imanena kuti: “Wina apweteka mnzake pomulamulira.”

Ngati Mulungu sanalole kuipa kwawo, ngati iye analoŵereramo ndi mphamvu kuti akuletse iko, kuimba kwa kudandaula kuti maufulu awo anali kusokonezedwa kukanakwera kufikira kumwamba! Iwo m’chenicheni amamfuna iye kulola kuipa kwawo kwaumwini, koma iwo amafuna kukhala okhoza kufesa iko popanda kututa zotulukapo zake.—Agalatiya 6:7, 8.

Oterowo amasoŵeka kuwona mtima ndi kudzichepetsa kwa Yobu, yemwe analapa pamene anamvetsetsa kuti Yehova sanali magwero a m’masoka ake. Chitaganya lerolino sichimayenda ndi Mulungu ndipo chotero chikututa masoka a njira yake, popeza “sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zaka zikwi za mbiri ya munthu zatsimikizira icho kukhala chowona.

Koma ichi chidzasintha mbadwo uwu usanathe, pamene Ufumu wa Kristu udzaloŵa m’malo dongosolo la kachitidwe ka zinthu la usatana. (Danieli 2:44; Mateyu 24:34; 2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Kenaka, ‘ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa,’ popeza Yehova Mulungu akunena kuti: “Tawona, ndichita zonse zikhale zatsopano.”—Chibvumbulutso 21:1, 4, 5; 2 Petro 3:13.

[Chithunzi patsamba 21]

Kalinde wa m’ndege Paul Garrett

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena