Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 9/8 tsamba 32
  • Kodi Mwana Wanu Ali ndi Kulembetsa Kwaumwini?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwana Wanu Ali ndi Kulembetsa Kwaumwini?
  • Galamukani!—1989
Galamukani!—1989
g89 9/8 tsamba 32

Kodi Mwana Wanu Ali ndi Kulembetsa Kwaumwini?

Kuti akulitse mwa achichepere awo chikhumbo cha kuphunzira, makolo anzeru amapangitsa mabukhu abwino kukhalapo kaamba ka iwo. Ambiri, mwachitsanzo, amatsimikizira kuti ana awo ali ndi kulembetsa kwaumwini ku magazini ya Baibulo Nsanja ya Olonda, yomwe imagwiritsiridwa ntchito monga maziko a kukambitsirana kwa Baibulo kwa mlungu ndi mlungu pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Koma kodi ndi pa msinkhu wotani pamene mwana afunikira kulandira kulembetsa kwaumwini?

Kalata yotsatirayi inalandiridwa kuchokera kwa mayi wina: “Kulembetsa uku ndi kwa mwana wathu wamwamuna wa zaka ziŵiri zakubadwa. Mkati mwa Phunziro la Nsanja ya Olonda, iye afunikira kukhala ndi kope lake. Ndayesera kumpatsa losiyanako pamene tinalibe kope lowonjezereka, koma iye ankazindikira kuti zithunzithunzi sizinagwirizane, ndipo anafuna kope limene tinalikugwiritsira ntchito. Ndiri wotsimikizira kuti zithunzithunzi zokongola zimakondweretsadi mwana wachichepere ndipo zidzathandizira chiyamikiro chake choyambirira cha chakudya chauzimu chimene panthaŵiyi angakhale sakumvetsetsabe.”

Bwanji osatsimikizira kuti aliyense wa ana anu ali ndi kulembetsa kwaumwini kwa Nsanja ya Olonda? Landirani kulembetsa kwa chaka chimodzi mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi K80.

Chonde tumizani Nsanja ya Olonda kwa chaka chimiodzi. Ndatsekeramo K80 (Zambia).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena