Mmene Ukwati wina Unapulumutsidwira
“Kugwiritsira ntchito uphungu wopezedwa mu bukhu la Kupangitsa Moyo Wabanja kunapulumutsa ukwati wanga,” analemba motero woŵerenga woyamikira wa ku South Africa. “Mutu 5, ‘Mkazi Amene Ali Wokondedwa Kwambiri,’ unatsegula maso anga. Sindinalingalirepo m’maloto anga onse oposapo kuti ndingapangitse mavuto ambirimbiri popanda kulingalira. Ndikuthokozani kwenikweni. Ukwati wanga unali m’mbali za namondwe zenizeni za nyanja, ndipo tsopano, pambuyo pa miyezi ingapo, iwo wabwereranso ku dokho lachimwemwe.”
Ngati mufuna thandizo la kupangitsa ukwati wanu kukhala wachimwemwe, mungapindule ndi bukhu limeneli. Landirani kope limodzi mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kali pansipa.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Ndatsekeramo K20 (Zambia).