Wosangalatsa Wofiirayo ndi Nyimbo Yosangalatsa
Kodi munagalamutsidwapo ndi nyimbo ya wosangalatsa wofiirayo? Ngati mumakhala mu North America, imeneyo mokondweretsa ingamakudzutseni kutulo chifukwa chakuti imodzi ya mbalame zodziŵika kwambiri zoimba nyimbo—cardinal—imamanga chisa chake m’chigawo chimenecho cha dziko. Cardinal yaimuna imakuta gawo lake ndi likhweru lomveka konsekonse. Ndipo ingakhale woimba wosatopa ndi wokhutiritsa. “Cardinal ina yaimuna inapezedwa kukhala ndi nyimbo 28 za mpangidwe wosiyasiyana,” ikutero The International Wildlife Encyclopedia.
Mbalame yokongolayi njapafupifupi masentimitala 20 muutali, yokongoletsedwa ndi nthenga zofiira ndi “kolala” yakuda kuzungulira mlomo wake. Komabe, yaikazi iri ndi thenga zofiirira. Iyo ndiimodzi yamagulu oŵerengeka a mbalame zimene zazikazi zake zimaimba.
Ziribe kanthu ndi kumene mumakhala, nthaŵi yotsatira imene mudzamva nyimbo yabwino ya mbalame, yamikirani Mlengi wanu wakumwamba kaamba ka nzeru zake ndi mphamvu zodabwitsa. Mbalame zoimba ndizo imodzi ya mphatso zake za mtundu ndi chisangalalo.—Salmo 148:7-10.