Tsamba 2
Kwa zaka mazana ambiri Spanya ndi Chikatolika zawonekera kukhala zosalekanitsika mofanana ndi Mariya ndi khandalo. Kucheza kwachipambano kwa papa ku Spanya mu 1982, mkumene mamiliyoni ambiri analandira John Paul II ndi mawu akuti Totus tuus (Zonse nzanu), anatsimikizira poyera kudzipereka kwa dzikolo ku chipembedzo chake cha makolo.
Koma chisangalalocho chitazirala, kutsutsana kosalekeza kunakhalapobe—kwina nkwakalekale, kwina nkoyambira m’nthaŵi yathu. Nkhani zotsatirapozo zidzasanthula kwina kwa kutsutsana kumeneku limodzi ndi zochititsa zake ndi matanthauzo awo kwa tchalitchi Chachispanya champhamvuyonse panthaŵi ina.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Agencia EFE