Kodi Baibulo Liri Kokha Bukhu Lina?
Ngati nditero, nchifukwa ninji ilo lawukiridwa mowopsya chotero m’mbiri yonse? Kodi mungalikhulupirire Baibulo? Kodi zozizwitsa zolembedwamo zinachitikadi? Kodi sayansi yatsimikizira Baibulo kukhala lolakwa?
Mayankho a mafunso ameneŵa ngofunika kwambiri, popeza kuti Baibulo limaneneratu za chiwonongeko cha dziko chomayandikira ndipo limapereka njira yopulumukira. Bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? lidzakupatsani mayankho okhutiritsa. Tumizani K20 yokha kaamba ka kope lanu laumwini.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 192 lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? Ndatsekeramo K20(Zambia).