Malo Otizinga Omanyonyotsoka
‘Ngati chinachake sichichitidwa, tingayembekezere kugwa kwa zachuma kofalikira ndi chipwirikiti cha makhalidwe’
NDIWO unali uthenga wa Lester Brown, prezidenti wa Worldwatch Institute, gulu lofufuza m’malo. Ndemanga zake zinatuluka mu lipoti lapachaka la “state-of-the-world” (mkhalidwe wa dziko).
Brown adati, malo otizinga adziko lapansi akupitirizabe kunyonyotsoka. Pokhapo ngati ziwopsyezo za kutha kwa mpweya wa ozone, chilala, kudula mitengo, kukokoloka kwa nthaka, ndi kuchuluka kwa anthu zichepetsedwa, “kugwa kwa zachuma kudzakhala kosapeweka.” Iye anadziŵitsa kuti kutulutsa chakudya kwa dziko lonse kwatsika ndi 14 peresenti pa munthu aliyense chiyambire 1984 ndikuti nkhokwe zambewu zakhala pa mlingo wotsikiratu kwa zaka 15.
Brown adanenanso kuti: “Nthaŵi siikutilola. . . . Tiyenera kuchitapo kanthu mkati mwa m’ma 1990. Kupyola apo kudzakhala kuchedweratu. . . . Ngati tidzakhala ndi kukolola kwina kwachilala kudzatigalamutsa modzidzimutsa. Pamenepo tidzakhala opanda mbewu zogulitsa ku maiko ena, ndi kuwirikiza kaŵiri kapena katatu kwa mtengo wa mbewu. Vuto la zachuma lidzapangitsa kupereŵera kwa mafuta kuwoneka ngati zamasewera.” Ananenanso kuti: “Kwa maiko ena amu Africa achedwa kale. Kulibe njira yosinthira zimenezi kumeneko. . . . Mothekera Latin America idzakhala yotsatira.”
Zochitika zimenezi zimagwirizana ndi maulosi a Baibulo amene amalankhula za njala, matenda, nkhondo, ndi imfa, ndi munthu “akuwononga dziko” m’nthaŵi yathu. Yesu ananeneratu kuti zimenezi zikathera mu “masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko.” Chimenecho chidzatanthauza mapeto a dongosolo iri lazinthu, kuyeretsa njira kaamba ka dziko latsopano la kakonzedwe ka Mulungu.—Chibvumbulutso 6:1-8; 11:18; Mateyu 24:21; 2 Petro 3:10-13.