Kodi Baibulo Liri Kokha Bukhu Lina?
Ngati nditero, nchifukwa ninji ilo lawukiridwa mowopsya chotero m’mbiri yonse? Kodi mungalikhulupirire Baibulo? Kodi zozizwitsa zolembedwamo zinachitikadi? Kodi sayansi yatsimikizira Baibulo kukhala lolakwa?
Mayankho a mafunso ameneŵa ngofunika kwambiri, popeza kuti Baibulo limaneneratu za chiwonongeko cha dziko chomayandikira ndipo limapereka njira yopulumukira. Bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? lidzakupatsani mayankho okhutiritsa.
Iyi ndi mbali ya ntchito ya kuphunzitsa Baibulo ya dziko lonse imene imachilikizidwa ndi zopereka mwaufulu.