Kodi Mulungu Amaloleranji Mavuto?
Mbiri yoipa iri chochitika chenicheni m’moyo, koma kodi nchifukwa ninji iri yofala motero? Kodi nchifukwa ninji pali mavuto ochuluka motero? Kodi kukhalapo kwake kungagwirizanitsidwe motani ndi kukhulupirira Mulungu wachikondi? Kodi mavuto adzatha konse?
Mayankho amafunso ameneŵa ndi ena ofunika kwambiri akupezeka m’Baibulo. Mayankhowo amaphatikizapo inu ndi banja lanu. Amaphatikizapo chimwemwe chanu. Buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi limapereka chiyembekezo mwakukusonyezani mayankho a Baibulo.
Masamba 256 a bukulo, aukulu wa magazini ano, adzaza ndi zithunzithunzi zophunzitsa zoposa 150, zambiri nzamawonekedwe okongola. Ngati mungafune kulandira kope, chonde lembani ndikutumiza kapepala kali pansipa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
U.S. Army