Tsamba 2
“PAFUPIFUPI munthu mmodzi mwa asanu a nzika za dziko lapansi ngachichepere a pakati pa zaka 15 ndi 24.” Inachitira lipoti tero UN Chronicle. Kunayerekezedwa kuti kuchiyambi kwa zaka khumi zino, chiŵerengero cha achichepere m’dziko chinafika pa mamiliyoni chikwi chimodzi! Achichepere amakono ngwosasowa—uku kuli magwero amphamvu ozindikiridwa nawo.
Psychology Today inachitira lipoti kufufuza kochitidwa pa achichepere 6,000 m’maiko khumi osiyanasiyana. Kunapezedwa kuti mosasamala kanthu za kusiyana m’zachuma ndi mwambo, achichepere amasonyeza zikhoterero ndi makhalidwe omwe “ali ofananana modabwitsa.” Kuchokera ku kufufuza koteroko kwatuluka chithunzi cha padziko lonse cha achichepere amakono, ndipo chomwe chikuvumbulidwa ndi ichi chingakudabwitseni zedi.