Minkhole Yopepuka ya Fodya
LIPOTI la Dokotala Wamkulu Wotumbula la mu 1989 likusonyeza kuti munthu atayamba kusuta ali wamng’ono kwenikweni, kumakhala kwachidziŵikire kwenikweni kuti iye adzafa ndi kansa ya mapapo. “Osuta fodya amene amayamba pambuyo pa zaka 25 ali ndi mlingo wakansa ya m’mapapo kuwirikiza nthaŵi 5 kuposa osasuta fodya; osuta fodya oyambira pa msinkhu wa zaka 20 ndi 24 ali ndi mlingo wapamwamba wowirikiza nthaŵi 9. Osuta fodya oyambira pamsinkhu wa zaka 15 ndi 19 ali ndi mlingo wapamwamba wangozi kuwirikiza nthaŵi 14 ndipo omwe amayamba asanafike msinkhu wa zaka 15 ali ndi mlingo wapamwamba wangozi kuwirikiza nthaŵi 19 kuposa osasuta fodya.”
Kaŵirikaŵiri kusuta fodya kumakhala kuyamba kulowa pamsewu wonkira ku mankhwala ogodomalitsa. Achichepere azaka zapakati pa 12 ndi 17 amene amasuta fodya anapezedwa ndi kuthekera kwa kugwiritsira ntchito mbanje kuwirikiza nthaŵi 10 ndipo ndi kuthekera kugwiritsira ntchito cocaine, hallucinogens, kapena heroin kuwirikiza nthaŵi 14. Kufufuza kwambiri kukusonyeza kuti zidakwa zoposa maperesenti 90 ndi omwerekera ndi heroin ndi osuta kwambiri.
Kufufuza kwaposachedwapa kwa Gallup kunasonyeza kuti 64 peresenti ya achichepere anakonda kuti fodya aletsedwe kwa amsinkhu wa zaka zapansi pa 21 ndikuti “chitsutso chapadera chokha ku malamulo oterowa opangidwa ndi mabungwe chimachokera kwa achikulire amene amapanga ndalama m’kugulitsa fodya kwa achichepere.”—Psychiatric, Mental Health, and Behavioral Medicine News Update, March-April 1990, tsamba 1.