“Bokosi la Chuma cha Mafunso ndi Mayankho”
Umu ndimmene mkazi wa ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A., analitchela bukhu lakumanja la Kukambitsirana za m’Malemba. Iye analongosola kuti: “Posachedwapa Mboni za Yehova ziŵiri zinabwera panyumba panga. . . . Mmodzi wa iwo mosadziŵa anasiya bukhu lamutu wakuti Kukambitsirana za m’Malemba. Kunena zowona, ndinamwerekera m’bukhulo! Ndinakhala pansi ndikuliŵerenga kwa maola ambiri. Ndinasangalatsidwa kwenikweni. . . . Bukhuli linali ngati bokosi la chuma cha mafunso ndi mayankho kwa ine, ambiri amene ndadzifunsapo ndekha.”
Bukhu la kumanja lofunika kwambiri limeneli njodzala ndi mitu yaikulu yoposa 70. Kuphatikizapo “Kutaya Mimba,” “Mankhwala,” “Maholide,” “Kutengedwa m’Thupi,” “Kudziveka Thupi Lanyama,” “Kugonana,” ndi “Kulambira Mizimu.” Zisonyezero zake za nkhani zamasamba asanu ndi aŵiri ndi malemba zingakuthandizeni kupeza mayankho mofulumira. Kuti mulandire kope, chonde dzazani ndikutumiza kapepala kali pansipa.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 448 la Kukambitsirana za m’Malemba. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 4.)