Tsamba 2
Dziko lathu lapansili ndiwo mudzi wa mabanja onse a anthu. Anthu onse amakhala pamodzi mu ilo ndipo amagawana zofunikira zazikulu ndizikhumbo zimodzimodzi.
Komabe, kugwirizana kwa mafuko sikunakhalepo kwalamulo pachiundachi. Mmalomwake, kaŵirikaŵiri kusiyana kwa anthu ndiko kumalamulira unansi wa anthu. Kwa zaka mazana ambiri kukangana kwabuka pankhani zokhudza fuko. M’kope lino la Galamukani!, tidzakambapo pa chimene chikudziŵika tsopano ponena za fuko ndi chifukwa chake tingayembekezere kuti padzakhala mapeto a kukangana konse kwa mafuko.