Kodi Iwo Amamamatira Kuzonena Zawo?
PAMENE kadinala wa Roma Katolika, John O’Connor anasonyeza kuti andale zadziko Achikatolika angachotsedwe ngati sachilikiza kaimidwe ka tchalitchi pa kuchotsa mimba, katswiri wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala Mike Royko analemba kuti: “Pakali pano, tiri ndi wansembe [Vincent Gigante] amene akupita kukhoti namanena kuti mmodzi wa apandu odziŵika kwambiri a mu New York, yemwe ntchito yake nkulanda anthu moŵawopseza, sali kwenikweni mpandu konse.”
Royko anawonjezera kuti: “Sindinaŵerengepo chirichonse chonena za O’Connor kukhala akulengeza kuti: ‘Aliyense wogwirizana ndi banja laupandu—kavalidwe ka Genovese, kulanda kwa Gambino ndi ena onsewo—adzachotsedwa. Chenicheni chakuti winawake anakhala chiŵalo cha tchalitchi chathu adakali wamng’ono sichimatanthauza kuti tiyenera kulekerera mkhalidwe wake woipa pamene akhala Ngwazi.’”