Chidziŵitso pa Nyuzi
Khomo Loloŵera ku Moyo Wakalewo?
Miyezi ingapo yapitayo, asungwana atatu apasukulu ya pulaimale ndi sekondale anapezedwa ogona pamsewu atakomoka m’Tokushima, Japan, chotulukapo cha kuyesa kudzipha. Kodi nchiyani chinapangitsa kachitidwe kawoko? Asahi Shimbun ikupereka lipoti lakuti: “Iwo anakhulupirira kuti anali ovala matupi anyama kuchokera kukukhala akalonga akale ndipo anadzikhutiritsa kuti angasunzumire m’moyo wawo wakale ngati anafika pamphembenu pa imfa.” Kumbuyo kwa chochitika chimenechi, ikutero nyuzipepalayo, kuli “chizoloŵezi pakati pa ana chakubwerera kuloŵa m’dziko losawoneka, [chimene] chafalikira mokulira mkati mwa zaka zingapo zapitapo.” Asunganawo anali okondetsa kuŵerenga mabuku osangalatsa ofotokoza zakuvala thupi lanyama.
Komabe, kulandira lingaliro la kuvala thupi lanyama kuli kopanda pake mofanana ndi kuthamangira chizimezime cha dzuŵa m’chipululu. Baibulo limavumbula kuti pa imfa ‘munthu amabwerera ku nthaka yake, ndipo tsiku lomwelo zolingirira zake zitaika.’ (Salmo 146:4) Chowonadi chimenechi chonena za imfa chaphimbidwa ndi chiphunzitso chonyenga chakuti moyo umapulumuka pa imfa ya munthu. Mmalo mwakuphunzitsa kuti anthu ali ndi moyo wosakhoza kufa, Baibulo limanena kuti moyo umafa. (Ezekieli 18:4) Koma kwa awo okhala m’chikumbukiro cha Mulungu, pali chiyembekezo chachikulu chachiukiriro. (Yohane 5:28, 29) Baibulo limavumbulanso wochititsa wamkulu wa ziphunzitso za moyo wosakhoza kufa ndi kuvala thupi lanyama; iye ndiye Satana Mdyerekezi, ‘atate wa bodza.—Yohane 8:44; yerekezerani ndi Genesis 3:4.
Akatolika ndi Kuchotsa Mimba
Pafupifupi zaka khumi zapitapo chiyambire kuperekedwa kwa lamulo pa kuchotsa mimba m’Italy kumene kunagonjetsa Tchalitchi Chakatolika. Komabe, m’kalata yoperekedwa posachedwapa ndi abishopu a ku Italy, ulamuliro Wachikatolika ukutchulanso kuti “kukana kuchotsa mimba kapena ngakhale kuthandizira kutero kumapereka thayo lalikulu loopsa, lozikidwa m’lamulo lolembedwa pamtima wa munthu ndikutsimikiziridwa ndi lamulo la tchalitchi, chimene chimapereka chilango chakuchotsedwa kwa Akristu omakuchita kapena okuthandizira.”
Kodi anthu a ku Italy amalingalira motani ponena za kuchotsa mimba? Mafufuzidwe aposachedwapa ophatikizamo anthu 2,040 anavumbula kuti mosiyana ndi zonena za tchalitchi, anthu a ku Italy amavomereza kuchotsa mimba m’mikhalidwe inayi. (1) Ngati mimba ikuika pachiswe moyo wa mayiyo, 83 peresenti amayanja kuchotsa mimba. (2) Ngati pali upandu wa kupunduka kwa mluza, 76.3 peresenti amayanja kuchotsa mimba. (3) Ngati thanzi la mkaziyo liri paupandu, 71.1 peresenti amayanja kuchotsa mimba. (4) Ngati mimbayo inakhala mwakugwiriridwa chigololo, 55.2 peresenti amavomereza kuti kuchotsa mimba kuloledwe. La Repubblica ikuchitira lipoti kuti, anthu a ku Italy oposa mmodzi mwa 4 amayanja kuchotsa mimba “m’mikhalidwe iriyonse pamene mkazi akufuna.” Chiŵerengero choyerekezeredwa cha kuchotsa mimba kwalamulo ndi kosaloledwa ndi lamulo cha 300,000 chimachitidwa chaka chirichonse mu Italy.
Nzowonekeratu kuti m’nkhani zovuta zoterezi, ulamuliro Wachikatolika walephera kupereka mokwanira chilangizo chake Chamalemba chokhulupirika kuchirikiza kukhulupirika kwawo. Komabe, Akristu owona aphunzitsidwa zimene Malemba amanena pankhani yofunika kwambiri imeneyi. Kaamba ka ulemu ku ziyeneretso zamakhalidwe abwino apamwamba Abaibulo, iwo samachotsa mimba mwa iriyonse ya mikhalidwe yolongosoledwa pamwambapo.—Eksodo 21:22-25; onaninso Salmo 139:14-17; Yeremiya 1:5.