Vuto la Kutaya Mimba Kodi Kupha Miyoyo 60 Miliyoni Ndiko Yankho?
ATASOKONEZEKA maganizo, ali wamantha, misozi ili mbwembwembwe, msungwana wa zaka 15 zakubadwa akuyang’ana bwenzi lake likuchokapo moipidwa. Mnyamatayo anamunena msungwanayo kuti ngwopusa chifukwa anatenga pathupi. Msungwanayo anaganiza kuti anali kukondana.
Mkazi wina wataya mtima pamene azindikira kuti ali ndi pathupi pa mwana wachisanu ndi chimodzi. Mwamuna wake ali paulova, ndipo anawo amagona ndi njala usiku uliwonse. Kodi iwo angasamalire motani mwana wina?
“Sizingachitike panthaŵi yoipa motere,” mkazi wovala bwino akufotokozera dokotala wake. Iye walandira digiri ya uinjiniya ndipo ali pafupi kuyamba ntchito yake yatsopano. Mwamuna wake ngwotanganitsidwa kwambiri ndi ntchito yake yauloya. Kodi akaipeza kuti nthaŵi yosamalira mwana?
Anthuwa ngosiyana kwambiri m’mikhalidwe yawo ya moyo ndipo akuyang’anizana ndi mavuto osiyana, koma akusankha yankho limodzi: kutaya mimba.
Kutaya mimba ndinkhani imodzi yovuta kwambiri ya m’zaka khumi zino, yomwe ikudzutsa mikangano m’zandale, mayanjano, zamankhwala, ndi maphunziro azaumulungu. Mu United States, ochilikiza moyo amamenyera zoyenera za mwana wosabadwayo. Gulu la ochilikiza chosankha limaumirira pa maziko alamulo a ufulu ndi kuyenera kwa mkazi kupanga chosankha. Ochilikiza moyo amalimbana ndi ochilikiza chosankha m’masankho, m’mabwalo amilandu, m’matchalitchi, ngakhale m’makwalala.
Mamiliyoni ena amitima iŵiri amagwidwa mkati mwa kulimbana kumeneku, ogaŵika pakati ndi zigomeko zotokosa maganizo za mbali zonse ziŵiri. Mawu enieniwo akuti “ochilikiza chosankha” ndi “ochilikiza moyo” anasankhidwa mosamalitsa kunyengerera anthu amitima iŵiri. Mu mbadwo uno umene ufulu umalambiridwa, kodi ndani amene sangayanje chosankha? Komanso, kodi ndani amene sangayanje moyo? Magulu ochilikiza chosankha amasonyeza mawaya okolowekako zovala kuchitira chitsanzo imfa za akazi oponderezedwa amene amataya mimba mwa njira zopanda chisungiko zosakhala zalamulo. Ochilikiza moyo amasonyeza majagi okhala ndi ana osabadwa otayidwa monga chokumbutsa chomvetsa chisoni cha osabadwa mamiliyoni ambiri akufa.
Tsoka lakupha lonseli likulongosoledwa bwino ndi Laurence H. Tribe m’buku lake lakuti Abortion: The Clash of Absolutes. “Ambiri amene angakhoze kuzindikira kuti mwana wosabadwayo ndimunthu, amene angamulingalire kukhala wofunika ndi kumlira, amangowona mkazi wapakatiyo ndi vuto lake. . . . Ena ambiri, amene amawona mkazi wapakatiyo ndi thupi lake, amene amaumirira kuyenera kwake kwakulamulira chotulukapo chake, amangowona mwana wosabadwa wokhala m’mimba mwa mkaziyo ndipo samalingalira moyo wake umene angaloledwe kukhala nawo kukhala weniweni.”
Pamene nkhondo yamakhalidwe imeneyi ikumenyedwa, ana osabadwa 50 miliyoni mpaka 60 miliyoni adzaphedwa chaka chino.
Kodi muli kumbali iti pankhani yosautsa maganizoyi? Kodi mungayankhe motani mafunso ovutawa: Kodi mkazi ali ndi kuyenera kwakukulu kwakusankha? Kodi kutaya mimba kungalungamitsidwe pansi pa mikhalidwe iliyonse? Kodi moyo umayamba liti? Ndipo funso lalikulu, ngakhale kuti silimafunsidwa kaŵirikaŵiri ndilakuti: Kodi Mlengi wa moyo ndi kubala ana amakuwona motani kutaya mimba?
Kutaya mimba kunayamba kale kwambiri. M’Girisi ndi Roma wakale, kutaya mimba kunali kofala. Ku Ulaya mkati mwa Nyengo Zapakati ndi Kubadwanso kwachidziŵitso, kutaya mimba kunali kuvomerezedwa kufikira panthaŵi imene mayiyo anayamba kumva kuyendayenda kwa khanda m’mimba mwake. Kufika kwa chipanduko cha m’zakugonana kunabweretsa zotulukapo zake—mimba zosafunidwa mamiliyoni ambiri.
Ma 1960 anayambitsa kuchuluka kwa magulu omenyera zoyenera za akazi, omwe kuyenera kwa kubala ndiko chifukwa chawo chachikulu. Ena amachilikiza kuyenera kwa kutaya mimba kwa mikhole ya kugwiriridwa chigololo kapena kugonana kwapachibale kapena pamene thanzi la nakubala lili paupandu. Luso lazamankhwala latheketsa kuwona mavuto omwe adzachitika pakubala ndi kudziŵa ngati mwanayo adzakhala wamkazi kapena wamwamuna. Mimba zimatayidwa kudalira pa mapendedwe a dokotala osonyeza zotsatirapo zoipa. Akazi okhala ndi zaka zakubadwa zoposa 40 angawope zilema.
M’maiko okanthidwa ndi umphaŵi, akazi ambiri amene ali ndi njira zochepa zopeŵera kutenga mimba amadziwona kukhala osakhoza kusamalira ana owonjezereka. Ndipo mwakuwonjezera tanthauzo la liwu lakuti ochilikiza chosankha, akazi ena apakati amasankha kutaya mwana wosabadwayo chifukwa akuganiza kuti sinthaŵi yabwino yokhala ndi pakati kapena chifukwa adziŵa kuti mwanayo ndi wamwamuna kapena wamkazi ndipo sakumfuna.
Zigomeko zambiri zoperekedwa pankhaniyi zimakhudza funso la pamene moyo umayamba. Oŵerengeka amakaikira mfundo yakuti dzira lopatsidwa mphamvu ndi ubwamuna ndiselo lamoyo. Funso nlakuti, kodi nlamoyo monga chiyani? Monga minyewa chabe? Kapena monga munthu? Kodi mbewu ya mtengo wa mbaŵa ndimtengo wa mbaŵa? Pamenepo, kodi mwana wosabadwa ndimunthu? Kodi ali ndi zoyenera zalamulo? Kulimbana ndi mawu kumeneku nkosatha. Nzodabwitsa chotani nanga kuti m’chipatala chimodzimodzicho, madokotala angagwire ntchito zolimba kupulumutsa moyo wa mwana wobadwa masiku asanakwane ndipo komabe amapha mwana wosabadwa wamsinkhu wofananawo! Lamulo lingawavomereze kupha mwana amene ali m’mimba, koma ngati mwanayo saali m’mimba kuteroko kumatchedwa kuchita mbanda.
Zidandaulo zamphamvu kwambiri zopempha kuvomereza kutaya mimba mwalamulo zimachokera kwa akazi “aufulu” amakono amene ali ndi njira zosalekeza zopeŵera kutenga mimba kwenikweniko. Iwo amanena mwamphamvu za kuyenera kwa kubala, pamene kwenikwenidi asonyeza kale kuthekera kwawo kwakutenga mimba ndi kubala. Zimene amafuna kwenikweni ndizo kuyenera kwakuletsa kubala kumeneko. Chodzikhululukira chawo nchiyani? “Ndithupi langa!” Koma kodi ndithupi lawodi?
Abortion—a Citizens’ Guide to the Issues imalongosola kuti m’milungu 12 yoyambirira yakukhala ndi pakati, “mulu waung’ono wa minyewa yotamuka umakhala wosavuta kuuchotsa.” Kodi kutaya mimba kungawonedwe moyenerera monga “kuchotsa mnofu wa minyewa” kapena “kuthetsa chotulukapo cha kutenga mimba”? Kapena kodi mawu okometsera ameneŵa alinganizidwira kuchepetsa ululu wa chowonadi chenicheni ndi kutonthoza zikumbumtima zovutitsidwa?
Chidutswa chosafunidwa cha minyewa chimenecho ndimoyo womakula, wosangalala, wokhala ndi machromosome akeake okwanira. Mofanana ndi ulosi wa mbiri ya munthu, chimasonyeza tsatanetsatane wa munthu wapadera amene akuumbika. Wofufuza wotchuka profesa wa maphunziro a ana osabadwa A. W. Liley akufotokoza kuti: “Mwakuthupi, palibe nthaŵi imene timavomereza lingaliro lakuti mwana wosabadwa ali kokha chowonjezera ku thupi la nakubalayo. Polankhula za majini, nakubalayo ndi mwanayo ali anthu osiyana kuyambira pakutenga mimba.”
Mkhalidwe Wosasamala
Komabe, pokhala ndi mwaŵi wakutaya mimba mosavuta, ambiri amalingalira kuti palibe chifukwa chodzichinjirizira ku kutenga pathupi kosafunidwa. Iwo amasankha kugwiritsira ntchito kutaya mimba monga chitetezo chothetsera “ngozi” zilizonse zimene zimachitika.
Ziŵerengero zikusonyeza kuti msinkhu wa unamwali watsika m’zaka za zana lino. Chifukwa chake, ana aang’ono ali ndi kuthekera kwakubala ana. Kodi iwo akuphunzitsidwa za thayo lolemera limene limatsagana ndi mwaŵi umenewo? Munthu wamba wa ku Amereka amataya unamwali wake pofika msinkhu wa zaka 16, ndipo mmodzi mwa asanu amataya unamwali wake asanakwanitse zaka 13. Mbali imodzi mwa zitatu za amuna ndi akazi okwatira amapitirizabe chibwenzi ndi munthu wina kapena anachita tero kalelo. Kutaya mimba kumakopa anthu achiŵereŵere. Mofanana ndi pempho lakuvomereza mwalamulo uhule kotero kuti achepetse kufalikira kwa matenda a AIDS, kuvomereza mwalamulo kutaya mimba kungapange chizoloŵezicho kukhala chachisungiko m’zamankhwala, koma kwachititsa mkhalidwe wochititsa matenda amakhalidwe kufalikira kwambiri.
Mikhole ya Chiwawa Kapena Mkhalidwe?
Mosangalatsa, kufufuza kumasonyeza kuti mimba zotengedwa chifukwa cha kugwiriridwa chigololo nza apa ndi apo. Kufufuza kumodzi kwa mikhole 3,500 yotsatizanatsatizana ya kugwiriridwa chigololo ku Minneapolis, U.S.A., sikunapeze nkhani ndi imodzi yomwe ya kutenga mimba. Mwa kutaya mimba 86,000 kumene kunachitika ku dziko lomwe kale linali Chekosolovakiya, kokha 22 kunali chifukwa cha kugwiriridwa chigololo. Chotero, chiŵerengero chochepa kwambiri cha amene amafuna kutaya mimba amachita tero chifukwa cha kugwiriridwa chigololo kapena kugonana kwapachibale.
Bwanji za zolosera zochititsa mantha zakuti anawo adzabadwa ndi zilema zosachiritsika? Madokotala ena amafulumira kusonkhezera kutaya mimba pamene azindikira kuti padzakhala mavuto pakubala. Kodi iwo angatsimikizire kotheratu za mapendedwe awo? Makolo ambiri angatsimikizire kuti maulosi owopsa amenewo angakhale opanda maziko, ndipo ali ndi ana achimwemwe, athanzi kutsimikizira nkhaniyo. Ena amene amalingaliridwa kuti ali ndi ana opunduka ngachimwemwebe kukhala makolo. Ndithudi, peresenti imodzi yokha ya awo amene amafuna kutaya mimba mu United States amachita zimenezo chifukwa anauzidwa kuti mwana wosabadwayo adzakhala wolemala.
Komabe, m’nthaŵi imene mwakhala mukuŵerenga nkhaniyi, makanda osabadwa afa mazanamazana. Kodi zimenezi zikuchitika kuti? Ndipo kodi miyoyo ya oloŵetsedwamowo ikuyambukiridwa motani?
[Mawu Otsindika patsamba 25]
Nakubala: “Ndithupi langa!”
Mwana: “Ayi! Ndithupi langa!”