Imfa Zochititsa Mantha za Kutaya Mimba
MAKANDA osabadwa kuyambira pa 50 kufika pa 60 miliyoni amaphedwa chaka chilichonse mwakutaya mimba. Kodi mungayerekezere chiŵerengero chimenecho? Kungakhale kofanana ndi kuseseratu chiŵerengero cha anthu onse a ku zisumbu za Hawaii mlungu uliwonse!
Ziŵerengero zenizeni nzovuta kuzipeza chifukwa chakuti maboma ambiri samasunga zolembedwa zosamalitsa za kutaya mimba. Ndipo kumene kutaya mimba kumaletsedwa mwalamulo, akatswiriwo amangoyerekezera chiŵerengerocho. Koma kuŵerengera kwapadziko lonse kwa kutaya mimba kuli kotere:
Mu United States, kutaya mimba kuli opaleshoni yofala kwambiri yachiŵiri kwa kuchotsa lilakalaka. Chaka chilichonse, kutaya mimba koposa 1.5 miliyoni kumachitidwa. Unyinji waukulu wa akaziwo ngosakwatiwa—anayi mwa asanu. Akazi osakwatiwa amachotsa mimba zawo kuŵirikiza kaŵiri kuposa mmene amabalira, pamene kuli kwakuti pa avareji, akazi okwatiwa amabala kuŵirikiza nthaŵi khumi kuyerekezera ndi mmene amatayira mimba.
Mu Central ndi South America—maiko Achikatolika—malamulo oletsa kutaya mimba ngokhwima kwambiri kuposa kwina kulikonse m’dziko. Komabe, kutaya mimba kopanda lamulo kumachitidwa mofala, kukumachititsa mavuto owopsa athanzi kwa akaziwo. Mwachitsanzo, akazi a ku Brazil anataya mimba zokwanira mamiliyoni anayi chaka chatha. Oposa 400,000 a iwo anafuna chithandizo chamankhwala chifukwa cha zovuta zobukapo. Ku Latin America pafupifupi gawo limodzi mwa anayi a onse okhala ndi mimba amachotsa mimbayo.
Kudutsa nyanja ya Atlantic kumka ku dziko la Afirika, malamulo alinso okhwima. Zivulazo ndi imfa nzofala, makamaka pakati pa akazi osauka amene amafuna chithandizo cha asing’anga osavomerezedwa ndi lamulo.
Ku Middle East konse, maiko ambiri ali ndi malamulo okhwima olembedwa, koma kutaya mimba kumachitidwabe mofala ndi akazi amene amakhoza kulipira malipiro aakulu.
Maiko ambiri a Kumadzulo kwa Ulaya amavomereza kutaya mimba, maiko a ku Scandinavia amapereka ufulu waukulu. National Health Service ya ku Briteni inasunga zolembedwa za kutaya mimba kuyambira pamene kunavomerezedwa mwalamulo mu 1967. Bungwelo lawona kuŵirikiza kwa ziŵerengero za kutaya mimba limodzi ndi kuwonjezeka kwa ana apathengo, matenda opatsirana mwakugonana, uhule, ndi matenda ena ambiri akubala.
Kum’maŵa kwa Ulaya kukuchitika masinthidwe aakulu panthaŵi ino, moteronso malamulo onena za kutaya mimba. Kumene kunali ku Soviet Union, kutaya mimba kukuyerekezeredwa kukhala 11 miliyoni chaka chilichonse, chiŵerengero chachikulu koposa padziko lonse. Popeza kuti mankhwala oletsa kutenga mimba ngosoŵa ndipo mikhalidwe yachuma njosaukira, mkazi wamba m’chigawocho angachotse mimba zisanu ndi imodzi kufika pa zisanu ndi zinayi m’moyo wake.
Kum’maŵa kwa Ulaya konse chikhoterero chili cha kupeza ufulu. Chitsanzo chodabwitsa ndi Romania, kumene ulamuliro wakale unaletsa kutaya mimba ndi mankhwala oletsa kutenga pathupi kuti ulimbikitse kuwonjezera chiŵerengero cha anthu. Akazi anakakamizika kubala ana osachepera pa anayi, ndipo pofika 1988, nyumba zosungira ana amasiye za ku Romania zinasefukira ndi achichepere onyanyalidwa ndi makolo awo. Motero, kuyambira pamene boma lopandukalo linachotsa ziletso zimenezi mu 1989, ana atatu mwa anayi alionse amatayidwa, chimene chili chiŵerengero chachikulu kwambiri cha ku Ulaya.
Asia ali ndi chiŵerengero chachikulu kwambiri cha kutaya mimba. Dziko la People’s Republic of China, limene lili ndi lamulo lolimbikitsa mabanja kukhala ndi mwana mmodzi yekha ndi kutaya mimba kokakamiza, lili ndi chiŵerengero chachikulu cha kutaya mimba, limasimba kutaya mimba kokwanira 14 miliyoni pachaka. Ku Japan akazi amakometsera zifanizo zazing’ono ndi zidole pokumbukira ana awo amene anatayidwa. Anthuwo amachita mantha kwambiri ndi mibulu yoletsa kutenga mimba, ndipo kutaya mimba ndiko njira yaikulu yolinganizira banja.
Ku Asia konse, ndipo makamaka ku India, luso la zamankhwala lapangitsa mavuto aakulu kwa magulu omenyera zoyenera za akazi. Njira zonga ngati amniocentesis ndi ultrasound zingagwiritsiridwe ntchito kudziŵira ngati mwanayo ndiwamwamuna kapena wamkazi kuchiyambi kwenikweni kwa pathupipo. Anthu a Kum’maŵa amakonda kwambiri ana aamuna kuposa aakazi. Chotero kumene njira zodziŵira kuti kaya ndimwamuna kapena mkazi ndi za kutaya mimba zimapezeka mosavuta, ana aakazi osabadwa amatayidwa m’ziŵerengero zochuluka, kuchepetsa chiŵerengero cha akazi pochiyerekezera ndi cha amuna. Magulu omenyera kuyenera kwa akazi tsopano ali m’vuto lakupemphadi kuyenera kwa mkazi kutaya mimba ya mwana wake wamkazi wosabadwa.
Mmene Nakubala Amamverera
Mofanana ndi kuchiritsa kulikonse, kutaya mimba kuli ndi upandu ndi kupweteka kwake. Panthaŵi yokhala ndi pathupi kukamwa kwa chibaliro kumatsekeka zolimba kuti mwanayo akhale wosungika. Kukutamula ndi kuloŵetsako zipangizo kungakhale kopweteka ndi kosautsa. Kutaya mimba kochita kupopa kungatenge mphindi 30 kapena kuposapo, ndipo mkati mwa nthaŵiyo akazi ena amamva kupweteka kwambiri ndi kukokeka kwa minofu. Kutaya mimba kochititsidwa ndi mchere, munthu amakakamizidwa kubala nthaŵi isanakwane, nthaŵi zina mothandizidwa ndi prostaglandin, chinthu chimene chimayambitsa kubala. Kukwinyikako kungachitike kwa maola kapena ngakhale masiku angapo ndipo kungamapweteke ndi kusautsa maganizo.
Mavuto ochitika mwamsanga pambuyo pakutaya mimba amaphatikizapo kukha mwazi, kung’ambika kuchibaliro, kubooka kwa chibaliro, kuundana kwa mwazi, kuyambukiridwa moipa ndi mankhwala akupha ululu, kukomoka, malungo, kuzizira, ndi kusanza. Ngati mbali zina za mwanayo kapena nsapo zatsalira m’mimba pamakhala upandu waukulu wakudwala. Kutaya mimba kosatsirizika nkofala, ndipo opaleshoni ingafunikire kuchotsa minyewa yotsalira yomawolayo kapena chibaliro chenichenicho. Kufufuza kwa boma ku United States, Briteni, ndi dziko limene kale linali Chekosolovakiya kumasonyeza kuti kutaya mimba kumawonjezera mokulira kusabala, kutenga mimba kochitikira m’thumbo, kupita padera, kubala mwana wosakwana masiku, ndi zovuta zina pakubala.
Yemwe kale anali dokotala wamkulu wopanga opaleshoni wa ku United States C. Everett Koop ananena kuti palibe ndimmodzi yemwe amene “anafufuza zotulukapo zamaganizo kapena liŵongo la mkazi amene anatayapo mimba ndipo tsopano amafunitsitsa mwana koma sangathe kubala.”
Magulu amene anasankhidwa kufufuza za kutaya mimba anayenera kuphatikizapo Akristu achichepere odzisungira amene amakhalabe anamwali chifukwa cha kulemekeza kwawo moyo ndi malamulo a Mulungu. Magulu amenewo akanapeza kuti achichepere ameneŵa amasangalala ndi maunansi abwino, ulemu waumwini wokulira, ndi mtendere wamaganizo.
Mmene Mwana Wosabadwa Amamverera
Kodi zimamveka motani kwa mwana wosabadwa wosungika bwino m’mimba mofunda mwa mayi wake ndiyeno mwadzidzidzi kusautsidwa ndi chipangizo chakupha? Tingangoyerekezera kokha, popeza kuti nkhaniyo sidzasimbidwa konse ndi munthu wodziwonera yekha.
Kutaya mimba kochuluka kumachitidwa m’milungu 12 yoyambirira ya moyo. Panthaŵiyi mwana wosabadwa wamng’onoyo amayeseza kupuma ndi kumeza, ndipo mtima wake umagunda. Amafunya zala zake zakumapazi, kukunga nkhonya, ndi kupidiguka m’dziko lake lamadzimadzi—ndipo amamva kupweteka.
Ana osabadwa ambiri amakanganulidwa m’mimba ndi kuyamwidwa ndi chubu chokoka mpweya chokhala ndi nsonga yakuthwa. Kachitidweko kamatchedwa vacuum aspiration. Mphamvu yoyamwa yaikuluyo (kuŵirikiza nthaŵi 29 za mphamvu ya chiŵiya chosesera m’nyumba chotchedwa vacuum cleaner) imaduladula thupi laling’onolo. Makanda ena amatayidwa mwa dilation and curettage, mpeni wansonga yopindika wopalira m’mbali mwa mimbayo, kudula kamwanako nthulinthuli.
Ana osabadwa amsinkhu wa milungu 16 angafe ndi kutaya mimba kochitidwa ndi madzi amchere, kapena kuikidwa paizoni ndi mchere. Singano yaitali imaboola thumba lokhala ndi madzi a m’chibaliro, kuchotsamo madziwo, ndi kuikamo madzi oŵaŵa mchere. Mwanayo akamameza ndi kupuma, namadzaza mapapo ake anthetewo ndi madzi apaizoniwo, amapirikuta ndi kukomoka. Chotulukapo cha paizoniyo chimakhala kupsa kwa khungu la mwanayo, kumene kumalisiya litakungudzuka ndi kukhwinyata. Ubongo wake ungayambe kukha mwazi. Imfa yopweteka ingachitike mkati mwa maola angapo, ngakhale kuti nthaŵi zina ngati zowawa zakubala ziyamba tsiku lomwelo kapena pambuyo pake, mwana wamoyo koma womafa amabadwa.
Ngati mwanayo ngwamkulu kuti sangafe ndi njira zimenezi kapena zofanana nazo, pamatsala njira imodzi yokha—hysterotomy, opaleshoni yokhala ndi cholinga cholakwa, kupha moyo m’malo moupulumutsa. Mimba ya nakubalayo imatsegulidwa mwa opaleshoni, ndipo pafupifupi nthaŵi zonse amatulutsamo mwana wamoyo. Mwanayo angalire. Koma ayenera kulekedwa kuti afe. Ena amaphedwa dala mwakupuyitsa, kumiza m’madzi, ndi njira zina.
Mmene Dokotala Amamverera
Kwa zaka mazana ambiri asing’anga avomereza mawu onenedwa m’lumbiro lolemekezedwa la Hippocrates, limene limanena kuti: “Sindidzapereka kwa aliyense mankhwala akupha, ngakhale ngati ndapemphedwa, kapena kupereka uphungu wakupha, ndipo sindidzapatsa mkazi aliyense mankhwala owononga [oyambitsa kutaya mimba], koma ndidzakhala wopanda liŵongo ndipo ndidzachiritsa molemekezeka.”
Kodi ndikulimbana kwamalamulo kotani kumene kumayang’anizana ndi adokotala amene amathetsa moyo m’mimba? Dr. George Flesh akufotokoza nkhaniyo motere: “Pamene ndinayamba kutayitsa mimba monga wophunzira, sindinavutike nazo maganizo. . . . Kusautsidwa kwanga kunayamba pambuyo potayitsa mimba mazana ambiri. . . . Kodi nchifukwa ninji ndinasintha? Kuchiyambi kwa ntchito yanga, okwatirana ena anabwera kwa ine ndi kupempha kutaya mimba. Ndinalephera kutero chifukwa chakuti kuchibaliro kwa wodwalayo kunali kolimba. Chotero ndinampempha kuti akabwerenso mlungu wotsatira, pamene kuchibaliroko kukafeŵa. Okwatiranawo anabweranso nandiuza kuti anasintha maganizo awo. Ndinabadwitsa mwana wawo miyezi isanu ndi iŵiri pambuyo pake.
“Zaka zingapo pambuyo pake, ndinaseŵera ndi Jeffrey wachichepereyo m’dziŵe losambirira pa tennis club kumene makolo ake ndi ineyo tinali mamembala. Iye anali wachimwemwe ndi wokongola. Ndinachita mantha kulingalira kuti vuto la luso ndilo linandilepheretsa kupha Jeffrey. . . . Ndikhulupirira kuti kudula nthulinthuli mwana wosabadwa, kokha chifukwa chakuti mayi wake wapempha kutero, ndikachitidwe koluluzika kamene chitaganya chathu sichiyenera kukavomereza.”
Nesi amene analeka kuthandizira kutaya mimba anasimba za ntchito yake m’chipatala chotayira mimba: “Imodzi ya ntchito zathu inaphatikizapo kuŵerenga ziŵalo zathupilo. . . . Ngati msungwana abwerera kunyumba zidutswa za mwanayo zidakali m’chibaliro chake, pangakhale mavuto aakulu. Ndinkatenga ziŵalozo ndi kuziŵerenga chimodzi chimodzi kutsimikizira kuti panali mikono iŵiri, miyendo iŵiri, thunthu, mutu. . . . Ndili ndi ana anayi. . . . Panali mkangano waukulu umene ndinalephera kuuthetsa pakati pa ntchito yanga ndi moyo wanga. . . . Kutaya mimba ndintchito yovuta.”
[Chithunzi patsamba 28]
Ku Asia, kumene ana aamuna amakondedwa, madokotala amataya mimba za ana osabadwa aakazi zikwi zambiri
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi: Jean-Luc Bitton/Sipa Press
[Chithunzi patsamba 29]
Mtolankhani pa chiwonetsero cha kusakondwa chotsutsa kutaya mimba akujambula chithunzi cha mwana wosabadwa wamilungu 20 amene anatayidwa mwalamulo
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi: Nina Berman/Sipa Press
[Chithunzi patsamba 29]
Chiwonetsero cha kusakondwa chochilikiza kutaya mimba mu Washington, D.C., U.S.A.
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi: Rose Marston/Sipa Press
[Chithunzi patsamba 30]
Ku United States, akazi 4 mwa 5 amene amafuna kutaya mimba ngosakwatiwa