Kututa Zochuluka Kubweretsa Chisangalalo mu Taiwan
TAIWAN ndichisumbu cha makilomita 390 m’litali ndi makilomita 140 m’lifupi. Chokhala ndi anthu oposa 20,000,000, nchimodzi cha malo okhala ndi anthu ochulukitsitsa koposa m’dziko. Anthu ake ochulukawo amalankhula Chinese, kapena Mandarin Chinese monga momwe Akumadzulo amachitchera. Koma zilankhulo zambiri ndi zinenero zamafuko pafupifupi 13 zimalankhulidwanso kunoko.
Yokhala m’malo adziko otchedwa Tropic of Cancer, Taiwan ndi chisumbu chachonde kwambiri, ikumapereka zotuta zochuluka za mpunga ndi dzinthu zina mwakuti yakhala yogulitsa maiko ena zakudya. Komabe, kututa kwa mtundu wina kukudzetsa chisangalalo kwa okhalamo ndi phande. Uku ndi kututa kwauzimu kwa amene akuvomereza moyanja “mbiri yabwino ya ufumu.”—Mateyu 24:14, NW.
Kudzala Kochepa Koyambirira
Ntchito yofesa mbewu za chowonadi cha Baibulo mu Taiwan inayamba pafupifupi zaka 60 zapitazo, pamene woimira Watch Tower Society anabwera kuchokera ku Japan ndikupereka nkhani Zabaibulo mu Taipei, likulu lake. Mwamuna wachichepere wa ku Japan wotchedwa Saburo Ochiai anavomereza uthenga Waufumu ndipo mwamsanga anayamba kulankhula kwa ena ponena za uwo. Pambuyo pake, aminisitala anthaŵi zonse aŵiri ochokera ku Japan anazungulira pachisumbupo, nafesa mbewu za mbiri yabwino. Potsirizira pake, anaponyedwa m’ndende ndi akuluakulu ankhondo a ku Japan nataya miyoyo yawo chifukwa cha Ufumu wa Mulungu. Mbewu zambiri zimene anafesa zinamera mofulumira pakati pa fuko la Amis, koma panapezeka chisangalalo chochepa pakati pa anthu ambiri a ku China okhala ku gombe lakumadzulo la chisumbucho. Iwo ali Abudda kapena Atao ozama.
Ntchito yotuta mwauzimu mu Taiwan yapitirizabe kuchokera pa chiyambi chochepacho, kotero kuti lerolino chisumbucho chakhala munda wobala zipatso. Mwachitsanzo, m’zaka zisanu zapitazo, anthu 529 anabatizidwa, ambiri ochokera mwa anthu a ku China. Izi zinafikitsa chiŵerengero cha olengeza Ufumu pa chisumbucho pa chiŵerengero chapamwamba cha 1,552 mu 1989. Inde, Atao, Abudda, ndi Akristu mwadzina akuvomereza ku mbiri yabwino ndipo akuphunzira ponena za Yehova Mulungu! Koma kodi zimakhala motani kulankhula kwa anthu a makulidwe osiyanasiyana motero? Ndipo kodi pakhala zotulukapo zotani?
Kuvomereza Kwaulemu Kulimbana ndi Chikondwerero Chenicheni
Ntchito yolalikira mu Taiwan ponse paŵiri njofupa ndiyopereka chitokoso chifukwa chakuti anthu a ku China ngaulemu mwachibadwa. Mwachisawawa, amamvetsera kwa alendo mwaulemu. Pamene zofalitsidwa za Baibulo zigaŵiridwa, zimalandiridwa chifukwa cha mkhalidwe waulemu. Motero, aminisitala ena anthaŵi zonse agaŵira magazini ofika ku 300 kapena apeza masabusikripishoni 100 a magazini athu m’mwezi umodzi. Pazaka zambiri, Mabaibulo ambiri, mabuku, magazini, ndi matrakiti asiyidwa kwa anthu. Tsono, nchifukwa ninji kuwonjezereka kwa ofalitsa Ufumu kwakhala kochedwa?
Chifukwa chimodzi chimaloŵetsamo malingaliro a Confucius omwe aumba maganizo a anthu kwa zaka mazana ambiri. Mogwirizana ndi Confucius, munthu amene “mwakulemekeza Mizimu amaikhalira patali, anganenedwe kukhala wanzeru.”a Lingaliro lakuti munthu wanzeru samadziloŵetsa kwambiri m’kulambira mizimu kapena milungu. Chotero, ambiri angakhale olakalaka kudziŵa za uthenga Waufumu, koma ndi oŵerengeka omwe amafuna kudziloŵetsa m’phunziro Labaibulo. Kenakanso, ngakhale kuti anthu a ku China amakhulupirira m’mizimu yambiri ndi milungu, lingaliro la Mlengi wamkulukulu nlachilendo kwa ambiri a iwo. Ndiponso, anthu ofala a m’Baibulo monga ngati Abrahamu ndi Davide sangatanthauze chirichonse kwa iwo. Chotero, sikovuta kuwona chifukwa chake nthaŵi ndi kuleza mtima ziri zofunikira kaamba ka kuthandiza anthu kunoko kuti alandire Baibulo monga Mawu ouziridwa a Mulungu ndikukulitsa unansi waumwini ndi Mlengiyo, Yehova Mulungu. Komabe, ndi dalitso la Yehova, zoyesayesa zoterozo zimafupidwa.
Chochititsa Kuwonjezereka
Kwazaka zambiri, mipingo ya anthu a Yehova mu Taiwan inachitira misonkhano yawo m’maholo alendi. Chifuno chakukhala ndi malo osonkhanira oyenerera chinabweretsedwa ku chisamaliro cha akulu mumpingo wina pamene munthu wokondwerera ananena mawu akuti: “Ngati muli ndi chowonadi, mukuchitanji m’malo otereŵa? Bwanji osakhala ndi malo osonkhanira okhazikika?” Chotero ndichidaliro pa Yehova, mpingowo unayamba kufunafuna malo a Nyumba Yaufumu. Potsirizira pake, iwo anagula zipinda ziŵiri zolumikizana m’nyumba yaikulu, ndipo tsopano ali ndi Nyumba Yaufumu yabwino.
M’zaka zisanu ndi chimodzi zapitazo, Nyumba Zaufumu 11 zamangidwa kapena kugulidwa mu Taiwan. M’chochitika chirichonse, izi zatulukapo kututa kowonjezereka ndi chiŵerengero chachikulu cha opezeka pa misonkhano. Chitsanzo chimodzi chinali mpingo wa kummwera kwa mzinda wa Tainan. Mu 1981 mzinda waukulu umenewu wa anthu 600,000 unali ndi mpingo waung’ono umodzi wokha wa olengeza Ufumu 44. Mofunikira kaguluka kanaganiza zakumanga Nyumba Yaufumu yawoyawo. Ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzawadalitsa, abalewo ndi alongo anapita patsogolo ndi projekitiyo ngakhale kuti holoyo inali yodya ndalama pafupifupi $200,000. Ena anapereka golidi yawo ya chikole chaukwati; ena anasinthira kutsogolo maulendo awo akumaiko akutali. Aliyense mumpingo anachirikiza mokwanira. Pamene abale pa ofesi yanthambi ya Watch Tower Society anamva za projekitiyo, anaganiza zakumanga nyumba ya amishonale pa Nyumba Yaufumu, motero akugaŵana pakati mtengo wake. Holoyo inamalizidwa mkati mwa zaka ziŵiri. Chotulukapo? Podzafika nthaŵi imene Nyumba Yaufumuyo inatha, chiwonkhetso cha ofalitsa chinafika 74! Pakali pano, mipingo iŵiri, ndi chiwonkhetso cha ofalitsa 160, ikugwiritsira ntchito holo imeneyo, ndipo chiŵerengero cha pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu chimafika avareji pafupifupi 250. Mipingo iŵiriyo tsopano ikupanga makonzedwe akumanga Nyumba Yaufumu yachiŵiri.
Kututa Pakati pa Magulu Amafuko
Kututa pakati pa magulu amafuko pa gombe lakumadzulo kwa Taiwan kwapitirizabe kuyambira pachiyambi penipeni pa ntchito Yaufumu pa chisumbucho. Ena a anthu a fuko la Amis amene anaphunzira chowonadi poyamba zaka zoposa 50 zapitazo akadali okangalika. Mkati mwa zaka zambiri, akhala akukumana ndi zitokoso zambiri. Mkati mwa kuloŵera kwa anthu a ku Japan m’Nkhondo Yadziko ya II, iwo anafunikira kuphunzira Japanese. Pamene chisumbucho chinabwezedwa kwa China pambuyo pa nkhondo, anafunikira kuphunzira chinenero cha Chinese. Kuchiyambiyambi kwa ma 1960, anayang’anizana ndi chiyeso cha mtundu wina. Panthaŵiyo anthu otchuka ambiri a fuko la Amis anasiya gulu loyera la Yehova kapena anatsimikizirika kukhala osayenerera kuyanjana nalo. Mkati mwa zonsezi, kagulu ka Mboni zokhulupirika kanapitirizabe kutumikira Yehova. Ambiri a adzukulu a abale ndi alongo okalamba okhulupirikaŵa tsopano akupititsa patsogolo ntchito yolalikira.
Anthu a magulu ena amafuko apitanso patsogolo mwauzimu. Mwachitsanzo, pali gulu lokhulupirika la olengeza Ufumu pakati pa fuko la Bunun. Ena a makolo awo aposachedwepa anali apalu osaka mitu ya anthu. Anthuŵa tsopano akulalikira uthenga wamtendere wa Ufumu wa Mulungu. Mafuko a Lukai ndi Paiwan alandiranso umboni wabwino, ndipo ambiri mwa iwo apanga masinthidwe aakulu m’miyoyo yawo. Ba Chu Fu akukumbukira chokumana nacho chake, mwakumati:
“Ndinabadwira m’malo amapiri a Pingtung. Popeza kuti bambo ŵanga anali mfumu ya fuko la Lukai, anthu ankabweretsa mphatso za chakudya, motero sitinafunikire kugwira ntchito yolimba iriyonse. Chifukwa cha khalidwe lotereli, ndinakhala ndi mzimu wodzitama kwambiri. Ndinakhala ‘mfumu’ ya zigaŵenga zachichepere, ndikumaopsa anthu ndikumawalanda ndalama. Ndinkaopedwa m’mudzi mwathu. Pausinkhu wa zaka 22, ndinatenga mmodzi wa atsamwali anga aakazi kukhala mkazi wanga. Koma moyo wachisembwere ndi uchidakwa zinali zitazika mizu mozama mwa ine kotero kuti ndinapeza moyo waukwati kukhala wovuta kuchita nawo. Mwamsanga ukwati wathu unasweka, ndipo ndinabwerera ku moyo wanga wakale.
“Pafupifupi nthaŵi imeneyi, mkazi wanga anayamba kupezeka ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Sindinali wokondwerera ndipo ndinadzilingalira kukhala wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu. Komabe, monga chotulukapo cha zoyesayesa zachangu ndizowona mtima za mkazi wanga, mu 1973 ndinavomera kutsagana naye ku msonkhano wamitundu yonse mu Taipei. Tinakakhala ndi banja la Mboni. Kukoma mtima kwa mlongo wa ku Chinayo ndi mkhalidwe wosanyada zinandikhudza mokulira. Titabwerera kunyumba, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndikupanga kuyesayesa kowona mtima kwakusintha. Ndinabatizidwa mu 1974.
“Chiyambire pamenepo, pakhala ziyeso zambiri. Chimodzi chinali chakuphunzira kuŵerenga Chinese. Kumakhala ndekha kunalinso china. Chifukwa chakuti panalibe abale achikulire mwauzimu oyanjana nawo kapena ofunako thandizo, ndinalimbikitsidwa kudalira pa Yehova. Ndinaphunzira kukhala wodzichepetsa ndikumamatira ku gulu la Yehova. Chotulukapo? Lerolino, onse m’banja langa ngokangalika m’chowonadi. Ndiri ndi mwaŵi wakukhala mtumiki wotumikira mumpingowo, umene tsopano uli ndi ofalitsa achangu 60. Ngakhale kuti ndiribe luso lapadera lirilonse, Yehova wadalitsa ndikuchirikiza zoyesayesa zanga m’ntchito yotuta.”
Kututa Kukupitirizabe
Taiwan iri kokha kambali kakang’ono ka munda wadziko lonse. Komabe, mawu a Yesu akuti, ‘Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka,’ akukhalanso owona kunoko. (Mateyu 9:37) Chaka chatha, 4,534 anapezekapo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Ndipo pamene kututako kukunka kuchimake, antchito amene akhala akugwira ntchito zolimba mu Taiwan akututa ndi kufuula kwachisangalalo.—Yerekezerani ndi Salmo 126:5, 6.
[Mawu a M’munsi]
a The Analects, vii 20, monga momwe linatembenuzidwira ndi Arthur Waley, mu The Analects of Confucius, 1938, Vintage Books, New York.
[Mapu/Zithunzi patsamba 31]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
JAPAN
CHINA
TAIWAN
PHILIPPINES
[Zithunzi]
Nyumba Yaufumu yomangidwa posachedwapa pa ngombe lakummawa kwa Taiwan
Olengeza ufumu adzetsa chisangalalo kwa ambiri m’dziko losakhwimali