Nthaŵi Yabwino Koposa ya Moyo
Wachichepere wina wa ku Nigeria, Kumadzulo kwa Afirika, posachedwapa analemba kuti: “Poyamba, ndinkaganiza kuti nthaŵi yauchichepere inali nthaŵi yovuta koposa ya moyo wamunthu ndikuti nthaŵi yachimwemwe koposa inali pamene munthu ali ndi msinkhu wokhala tate kapena mayi kapena ali wamkulu.”
Koma kenaka wachichepere Wachifirikayu analandira kope la bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It. Iye analemba kuti: “Zikomo kwambiri. Bukhuli landithandiza m’njira zambiri.” Anamaliza kuti: “Tsopano, pambuyo poŵerenga bukhuli, ndazindikira kuti unyamata ndiyo nthaŵi yabwino koposa.”
Achichepere omakulira m’nthaŵi zovuta zino amayang’anizana ndi mikhalidwe yatsopano yambiri ndipo ayenera kupanga zosankha zamphamvu. Kodi wachichepere ayenera kusuta kapena kulandira mankhwala ogodomalitsa? Kodi ndi kachitidwe kotani kamene kali koyenera ndi wosiyana naye chiŵalo? Bwanji ponena za mphyotomphyoto ndi kugonana kwa ofanana ziŵalo?
Zosankha zolakwika zingatsogolere ku kupsinjika mtima kosiyanasiyana ndi mavuto. Your Youth—Getting the Best out of It limakambitsirana mafunso onse ali pamwambapo ndi ena owonjezereka. Ngati mungakonde kulandira kope, chonde lembani ndikutumiza kapepalaka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 192 la Your Youth—Getting the Best out of It. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)