Kodi Mudayamba Mwaganizapo?
◼ Kodi lingaliro la Mulungu nlotani ponena za chisudzulo?
◼ Kodi Baibulo limavomereza dama kapena kugonana kwa ofanana ziŵalo?
◼ Kodi nchifukwa ninji Mulungu wakulola kuvutika?
◼ Kodi iye adafunadi kuti dziko likhale chomwechi?
◼ Kodi mtsogolo mwasunganji?
Mmodzi wa Mboni za Yehova angakhale wokondweretsedwa kukuchezerani ndi kukuthandizani kupeza mayankho a Baibulo ku mafunso ameneŵa. Mboni za Yehova zimapereka chilangizo cha Baibulo kwa munthu payekha ndi cha gulu popanda malipiro.
Choncho ngati mungafune kuchezeredwa ndi munthu woyeneretsedwa panyumba panu, kapena pamalo ena oyenerera, tidzakhala osangalala kupanga makonzedwe. Mudzathandizidwa kupeza osati kokha mayankho a mafunso anu a Baibulo komanso mayankho a mavuto amene angathetsedwe mwakugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Kuti mupindule inu eni ndi utumiki umenewu, tangolembani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndinakonde kudziŵa zambiri ponena za Baibulo. Chonde pangani makonzedwe kuti winawake andifikire.